Vuto siinu a Malawi, vuto ndiife m’bomamu – Usi

Advertisement

…munthu wina akumathimitsa dala magetsi: awuza a Matola kuti asadzalireso

Wachiwiri kwa mtsogoleri wa chipani cha UTM, a Michael Usi, ati zinthu sizikuyenda bwino mdziko muno kaamba koti m’boma muli anthu ena oyipa, ndipo awuza nduna ya za mphamvu za magetsi ndi migodi a Ibrahim Matola kuti asadzalileso pankhani yakuthimathima kwa magetsi.

A Usi omweso ndi nduna ya zachikhalidwe amayankhula izi lamulungu pa 4 September pomwe chipani cha UTM chinachititsa nsonkhano pabwalo la zamasewero la Nyambadwe mumzinda wa Blantyre.

Malingana ndi a Usi, chipani cha UTM chinaitanitsa nsonkhanowu ndi cholinga chofuna kumva kuchokera kwa anthu otsatira chipanichi pankhani zomwe zikukhudza moyo wawo wa tsiku ndi tsiku.

Poyankhapo pamadandaulo omwe anthu anapeleka pa nsonkhanowu omwe ena mwa iwo ndikukwera mtengo kwa zinthu mdziko muno, a Usi anati a Malawi alibe vuto lili lonse koma akuluakulu aboma.

“Kumafunika kudziwa kuti mwana akagwa chamugwetsa nchiyani, osangofikira kumtukwana. Inu nonse a Malawi mulibe vuto, vuto lili ndi ife amene tili m’boma. Ngati pali anthu oti akonze siinu koma ndiife amene tili m’boma,” atelo a Usi.

Iwo anati ndizokhumudwitsa kuti pamene anthu ena m’boma ali kalikiliki kufuna kuthetsa mavuto omwe anthu mdziko muno akukumana nawo, kagulu kena ka anthu kaliso kalikiliki kuononga zinthu kuti pasakhale kusintha kuli konse.

Iwo anapeleka chitsanzo cha ku nthambi yowona zotuluka ndikulowa mdziko muno kuti kuli munthu wina amene akumasokoneza netiweki kuti ntchito yopanga ziphaso zoyendera isachitike ndipo ati izi sizoyenera.

A Usi ati palinso anthu ena ku kampani yogulitsa magetsi ya Escom omwe akumathimitsa mwadala magetsi ndipo ati pankhaniyi iwo anaitana anduna oyang’anira zamphavu a Ibrahim Matola kuti asadzalireso pankhani yokhudza kuthimathima kwa magetsi mdziko muno.

“M’boma muli anthu oyipa, ndikati kuipa ndikunena kuposa kuipa. Mwachitsanzo, pa 31 August, 2022,  ndinava kuti ku imigireshoni kuli anthu ambiri, ena akumagonera komweko, ndipo ntafufuza mnapeza kuti wina wake akungogwetsa netiweki.

“Mmene zikuchitikira zamagetsi, kungogwetsa magetsi phaa! Pamene anthu akuvutika. Ndiye mnava kuti a Ibrahim Matola, olemekeza anduna analira, nde mnawaitana ku ofesi, muzawafuse, mnawauza kuti musazalireso. Olira akhale othimitsa magetsiyo osati inu. Ngati kuthyola anthu, muthyole amene amathimitsa magetsiyo, osati inu muzilira iyayi,” anatelo a Usi.

Pofuna kutsindika kuti m’boma muli anthu oyipa mtima ngati mfiti zazikazi, a Usi anati akuluakulu ena mmaofesi aboma akumakhalira mapepala azitukuko ngakhale kuti zitukuko zina zikumakhala kuti mtsogoleri wadziko a Chakwera anazivomeleza kale.

Apa ndunayi inapeleka chitsanzo chankhani yofuna kukonzaso malo ochitira zisudzo a Blantyre Cultural Center, omwe sanakozedwebe mpaka pano ngakhale kuti mtsogoleri wa dziko lino anavomeleza za ntchitoyi kalekale.

Iwo apeleka maganizo oti ngati a Chakwera akufuna kuti zinthu zisinthe mdziko muno, akuyenera achotse onse omwe sakugwira bwino ntchito ndipo mmalo mwawo muikidwemo anthu atsopano omwe ali ndi chidwi pankhani yotukula dziko lino.

Wachiwiri kwa mtsogoleri wa UTM yu anatiso chipani chawo chinalibe maganizo oti chipusitse anthu ndi malonjezo omwe ena mwaiwo sakukwanilitsidwabe mpaka pano, koma ati vuto ndiloti akugwira ntchito limodzi ndi adani.

“Zikomo anthu aku Ndirande kuti mwabwera mwaunyinji. Uku ndikutitembelera ife kuti tinakunamizani. Ndikuuzani, panalibe kukhala pansi kuti tinamize anthu. Vuto la ifeyo tivomeleze, tikugwira ntchito ndi adani,” anateloso a Usi.

Iwo anatsindikanso kuti kupatula kukafotokozera a Chilima pazomwe anthu adandaula pansonkhanowu, ati akakumanaso maso ndi maso ndi a Chakwera kuti akawafotokozere madandowa.

 

Follow us on Twitter:

Advertisement