Chepetsani uchimo wa uchidakwa — Simama

Advertisement

Bishop Abraham Simama wa Mpingo wa Glorious Light International wa mzinda wa Lilongwe wadandaula ndi mchitidwe wauchidakwa omwe wachulukira pakati pa achinyamata mu dziko lino.

Poyankhula pa msonkhano wa tolankhani lachinayi, a Simama anati mpingowu waganiza zopanga
msonkhano wachinyamata omwe udzachitikire ku malo opembedzera ku Lilongwe.

A Bishop Simama adauza atolankhani kuti achinyamata amasikuano ali ndi makhalidwe osayenera omwe amapangitsa kuti asamapite kokapemphera chifukwa cha satana yemwe wamanga mizu komanso amene akuwalamulila.

Iwo anawochenjeza ponena kuti umphawi ndi chinthu china chomwe chikupangitsa achinyamata kuti akhale amakhalidwe osayenera zomwe zikuwapangitsa kuti asamalemekeze makolo awo omwe osati chifukwa chakulephera kwa makolowo koma chifukwa cha satana.

“Ife taona kuti tisakhale chete koma tichitepo kanthu nchifukwa chake taganiza zopanga msonkhano umenewo ndipo tikumema achinyamata kuti abwere posatengera Mpingo omwe amapemphera. Izitu si za achinyamata okha ayi komanso anthu amene Ali pabanja.

“Msonkhano umenewo uchitika kuyambira pa 3 mpaka 4 September. Ofuna kuti akapemphereredwe akupemphedwa kulembetsa kuti akhale mukaundula wa anthu omwe akuyenera kupemphereredwa kuti dzanja la ambuye likachite chozizwa pa iwo. Msonkhanowo ndi waulere,” anatero a Simama.

Iwo anatinso anthu ochokera m’mayiko ena akhala nawo pamsokhanowo ndipo ena mwaiwo abwera kale kuchokera mu dziko la Nigeria ndipo a Prophet achidzimayi otchedwa Yanka ndi Annie akuyembezeredwa kukhala nawonso pankumanowu.

A Simama adauza atolankhani wa kuti kupatula msonkhanowu, mpingowu udaganizanso zopereka zinthu za chifundo popereka zinthu ngati ufa ndi zina kwa mawanja okwana 1500 omwe amachokera mu mizinda ya Mchesi, Kawale, komanso Mtsiliza kuyambira pa 5 komanso pa 6 September.

“Mulungu akatidalitsa tikuyenera kudalitsanso ena kuti nawonso miyoyo yawo isinthe. Ife timakhalupira ku sintha miyoyo ya anthu ena chifukwa ukatero mulungu amakudalinsanso,” a Simam anawonjera potero.

Msonkhanowu uzachitika pa mutu ukuti “Yesu Nkhristu ndiye ngonjesi”.

Follow us on Twitter:

Advertisement