Sukulu ya apolisi yaoyendetsa galimoto yautsa mapokoso

Advertisement

Bungwe la sukulu zoyima pazokha zophunzitsa anthu kuyendetsa galimoto, lati ganizo loti nthambi ya apolisi m’dziko muno itsekule sukulu yophunzitsa anthu kuyendetsa galimoto, ndilolakwika ponena kuti liwaphera nsika.

Nkhaniyi ikudza pomwe posachedwapa nthambi ya polisi m’dziko muno yalengeza kuti ili kalikiliki ndimadongosolo ofuna kukhazikitsa sukulu komwe aziphunzitsa anthu kuyendetsa magalimoto amtundu osiyanasiyana.

Malingana ndi ofalitsa nkhani ku nthambi ya apolisi a Senior Superintendent Peter Kalaya omwe anayankhula nditsamba lino sabata yatha, maganizo otsekula sukuluyi adza ndicholinga chofuna kusula mashoveli apamwamba.

Senior Superintendent Kalaya anati izi zithandiza kuchepetsa chiwerengero cha ngozi zapansewu zomwe zimadza kaamba kosowa upangili okwanira kwa anthu oyendetsa galimoto.

“Tikukhulupilira kuti izi zitithandiza kuchepetsa ngozi zapansewu chifukwa oyendetsa galimoti akhala ndi upangili wapamwamba komaso nzeru zokwanira pakayendetsedwe komaso kasamalidwe ka galimoto zawo,” anatelo a Kalaya pouza Malawi24.

Koma patangodutsa maola ochepa nthambiyi italengeza zachiganizochi, bungwe la sukulu zophunzitsa anthu kuyendetsa galimoto mdziko muno la Driving School Association of Malawi (DRISAM), lati silosangalatsidwa ndiganizoli.

Malingana ndi mtsogoleli wa DRISAM a Gracious Madzi Odikha Kubwalo yemwe anayankhula ndi nyumba zina zoulutsa mawu mdziko muno, kukhazikitsidwa kwa sukuluyi, kuli ndi kuthekera koononga malonda a sukulu zawo.

“Ndife okhudzidwa kwambiri ndi maganizo a nthambi ya polisi oti itsekule sukulu yophunzitsa anthu kuyendetsa galimoto ndipo ife tikanakonda kuti ganizoli aliwunike bwino bwino sukuluyi isanakhazikitsidwe,” watelo Kubwalo.

A Kubwalo anati bungwe lawo la DRISAM likufuna lithamangile ku bungwe la Competitions and Fair Trading Commission (CFTC) kuti likafunse nzeru pa maganizo omwe nthambi ya polisiyi ili nawo kuti iyambitse sukulu ya oyendetsa galimoto.

Kupatula kukamang’ala Ku bungwe la CFTC, a Kubwalo ati gulu lawo liliso ndi chiganizo chofuna kutenga chiletso kubwalo la milandu ndicholinga choti ganizo la nthambi ya apolisili lisatheke.

Pakadali pano Senior Superintendent Kalaya ati nthambi ya apolisi ndiyodabwa ndikudandaulaku ponena kuti sukulu yawo izigwilira ntchito limodzi ndi sukulu zomwe sizabomazi ndipo ati nthambiyi ilibe ganizo lofuna kulanda nsika.

“Ife sitikufuna kulanda nsika, koma iyi ndinjira imodzi yofuna kuonetsetsa kuti m’misewu yadziko lino muli chitetezo chokwanira,” atelo a Kalaya.

Anthu ena omwe ayikira ndemanga pazankhaniyi m’masamba a nchezo, ayamikira nthambi ya polisi paganizoli ponena kuti zithandiza nthambiyi kuti izipeza ndalama zokwanira zoyendetsera ntchito zake mdziko muno.

Ngakhale zili choncho, anthu ena ali mbali imodzi ndi bungwe la DRISAM ponena kuti nthambi ya polisiyi ikuyenera kusiyira ntchito yophunzitsa anthu kuyendetsa galimoto mmanja mwa sukulu zomwe sizabomazi.

 

Follow us on Twitter:

Advertisement