Mpaseni dimba Chisaleyo: a Malawi ayamikira Kazembe wa Amerika

Advertisement
Anthu mdziko muno makamaka pamasamba a mchezo ayamikira komaso kudabwitsika ndi zintchito za kazembe wa dziko la Amerika a David Young omwe sabata ino anathandiza mayi wina kuphika mandasi ndipo analawanso mandasiwo.

A Young omwe anabwera mdziko muno mwezi wa March chaka chino, anatutumutsa anthu pomwe anayendera a Margaret Makhuza omwe amaphika mandasi ku Area 18 A mumzinda wa Lilongwe.

Kanema yemwe anthu akugawana m’masamba amchezo komaso waikidwa pa tsamba la fesibuku la ofesi ya kazembe wa mdziko la America, a Young akuoneka akutakataka kuwathandiza mai Makhuza kuphika mandasiwa.

Gawo lina lakanemayu likuonetsa kazembeyu akuwauza mayi Makhuza kuti; “ndimafuna ndilawe mandasi” ndipo atapatsidwa ndikudya, anayamikira ponena kuti; “mandasi okoma kwambiri,” zomwe zachititsa chidwi anthu ambiri.

Patsambali, kazembe Young wayamikira mayi Makhuza kuti amaphika mandasi opatsa mudyo ndipo kuyambira tsopano, mandasi chikhala chimodzi mwa zakudya zawo zokondedwa kwambiri.

“Potengera maganizo omwe mwakhala mukupeleka pankhani yoti ndizalawe chakudya chanji, sabata ino ndinayendera mayi Margaret Makhuza ku Area 18 A kuti ndikalawe mandasi awo okoma.

“Anthu aku Lilongwe akhala akukonda malonda awo kwa zaka zambiri ndipo ndachidziwa chifukwa chake. Anandiloraso kuti ndiyeseko kuphika mandasi ochepa. Ichi ndichakudya changa chokondedwa chatsopano. Zikomo kwambiri mayi Makhuza,” watelo Young.

Ndipo anthu ambiri omwe anaikira ndemanga pa kanemayu komaso zomwe tsambali linalemba, ayamikira a Young ponena kuti ntchito zawo ndizopatsa chikoka ndipo ena ati mkuluyu anakakhala mbeta anakamulimbikitsa kuti apeze kansoti komkuno.

“Big ndinu dolo. If you were single (munakhala osakwatira) tikanati kwatirani konkuno!!! Big Up (pitilizani),” anatelo a Ezekiel Peter Ching’oma poikira ndemanga pa kanemayo.

Mbali inayi, a Mphatso Shurkairy Zimtambila anati kazembeyu akuchita zinthu mosaonetsa tsankho kuti iye ndimzungu ndipo anati akufunika kuwapatsa mfundo ndipo anapeleka mfunda wa Chisale.

Aka sikoyamba kuti kazembeyu achite zinthu zopeleka chikoka kwa a Malawi kaamba koti mmezi wa June mkuluyu analimgulu la anthu omwe anachemelera mwa mtima bii timu yampira yadziko lino pomwe imasewera ndi Ethiopia pa bwalo la Bingu ku Lilongwe.

M’mwezi wa May, kazembeyu anatulutsa kanema yemwe amafotokoza za chidwi chake pofuna kuphunzira chikhalidwe cha ku Malawi ndipo mukanemayo, ngakhale a Young anali atakhala mdziko muno kwa masiku ochepa chabe, amayankhula chichewa.

Mukanemayo a Young anatsindikanso kuti ayesetsa kumapanga nawo zonse zomwe a Malawi amapanga.

 

Follow us on Twitter:

Advertisement