Nzika ya ku China yakhapa kasitomala ku Blantyre

Advertisement

Apolisi ku Limbe mu mzinda wa Blantyre amanga nzika ina ya dziko la China kaamba kovulaza mayi yemwe anadandaula kuti anamugulitsa belo la zovala zong’ambika.

Izi ndimalingana ndi ofalitsa nkhani pa polisi ya Limbe a Patrick Mussa omwe azindikira nzika yaku China yi ngati a Jiqo Chi Ping omwe ndimwini wake wa shopu ya Yibo ndipo anavulaza a Janet Phiri.

A Mussa anauza tsamba lino kuti sabata yangothayi a Phiri anagula belo la zovala za ana pa mtengo wa K280,000 ndipo anapita nayo ku malo awo ochitila malonda ku Thondwe m’boma la Zomba komwe amafuna akagulitse.

Nkhaniyi yati mayiwa atakatsekula beloli ku malo awo ochitira malondawa, anapeza kuti zovala zonse zomwe zinali mu beloyi zinali zong’ambika ndi zakutha zomwe zinawakwiyitsa ndipo loweruka pa 9 July ananyamuka kubwelera ku Limbe komwe anagula beloli.

Mayi Phiri atadandaulira a Chi Ping za kung’ambika kwazovala zomwe anazipeza mu belo ya zovala yi, mwini shopu yu anatenga chikwanje ndi ku khapa pamutu a Phiri zomwe zinapangitsa kuti ataye magazi ochuluka.

Atatsinidwa khutu za nkhaniyi, apolisi anathamangira ku malowa komwe anamanga a Chi Ping.

Pakadali pano mayi Phiri akulandira Thandizo la mankhwala pachipatala cha Queen Elizabeth mumzinda wa BlanBlantyre pamene a Chi Ping atsekulilidwa mlandu ovulaza munthu.

Advertisement