Ofuna kumwera nsuzi sasamba m’manja nsima isanathe – Chilima

Advertisement

Amene anali ndi chiyembekezo choti awona kugawana zida pakati pa chipani cha UTM ndi zipani zina mu mgwirizano wa Tonse ayembekeze kaye pang’ono kaamba koti a Saulos Chilima ati akufuna kumwera nsuzi ndipo sangasambe mmanja nsima isanathe.

A Chilima anayankhula izi lachisanu ku nyumba yawo ku Lilongwe komwe anapeleka malonje kwa khwimbi la anthu lomwe linakhamukira ku nyumbayi potsatira mphekesera yoti bungwe lothana ndi katangale la ACB likufuna liwafuse mafuso pankhani ya katangale.

Poyankhula ku khamu la anthuli, a Chilima anati mumchaka cha 2020 anauzidwa kuti akuyenera kudzichepetsa ndipo iwo ati anachita zomwezo pothetsa maganizo ofuna kudzakhala mtsogoleri wadziko lino ndipo m’malo mwake anavomera kukhala wapambuyo pa a Chakwera.

A Chilima omweso amathamangira kunkumano wa azitsogoleri azipani mumgwirizano wa Tonse omwe anaitanitsa ndi a Chakwera, anati kudzichepetsa komwe anapanga sikukutanthauza kuti iwo ndiopusa.

“Mu 2020 tinkanena kuti dzichepetseni, dzichepetseni, nde tadzichepetsa koma kudzichepetsako kusasanduke kufanana ndi kupusa,” anatero a Chilima poyankhula ndi gululo.

Koma pamene anthu ambiri amaona ngati chipani cha UTM chitha kutuluka mumgwirizano wa Tonse potsatira mphekesera zoti pali kusamwerana madzi pakati pa akuluakulu amgwirizanowu, a Chilima awonetsa kuti alibe malingaliro ngati amenewa.

Iwo anauza anthu omwe anasonkhana ku nyumba kwawoko mwambi omwe kutanthauzira kwake kukufanana ndikuti satuluka mumgwirizano wa Tonse ndipo adikira kaye mpakana kumapeto kwa zonse.

“Pachichewa pali mawu, akuluakuluwo amanena kuti; ofuna kumwera nsuzi sasamba mmanja nsima isanathe,” anatelo a Chilima.

Pophera mphongo kuti alibedi maganizo otuluka mgwirizano wa Tonse pano, a Chilima analangiza otsatira chipani cha UTM kuti apilire ponena kuti pamene akupita chitsogolo akumana ndi zinthu zosiyanasiyana ndipo anati ino ndi nthawi yake yoti zitelo.

Wachiwiri kwa mtsogoleri wadzikoyu wauzaso otsatira chipani cha UTM kuti sabata yamawa apeza tsiku loti awayankhuleso koma wapempha anthu onse kuti apitilire kusunga bata.

Chatsitsa dzaye kuti njobvu ithyoke mnyanga nchakuti a Chakwera alengeza kuti kuyambira pano sadziwapatsaso ntchito a Chilima kaamba koti atchulidwa ndi bungwe la ACB kuti alimugulu la anthu omwe anachitapo zakatangale ndi ochita malonda Zunneth Sattar.

Pakadali pano, a Chilima kudzera mumchikalata chomwe anatulutsa mkati mwasabatayi, akana kuti iwo sanachite za katangale monga momwe bungwe la ACB likunenera.

Follow us on Twitter:

Advertisement