Ndinanyula – Onesimus

…Chintuwi apempha kukhululukidwa

Advertisement

Onesimus wavomereza kuti ananyula usiku wa loweruka pomwe ananyoza amuna. Woyimbayu wati sadzayambiranso ndipo wapempha kuti anthu amukhululukire .

Woyimbayu yemwe ena amamuti Chintuwi watulutsa uthenga wake opepesa a Malawi.

Loweruka ku mwambo wa zoyimbayimba osangalala za mowa wa kuchekuche ku Lilongwe, Onesimus ananyogodola amuna omwe omwe sapatsa akazi awo ndalama ponena kuti amunawa ndi opanda ntchito.

Iye anatinso amuna omwe sawatengera akazi awo ku holide kapena kuwatenga kuti akagule zinthu kumashopu ndi opandanso ntchito.

Izi zinakwiyitsa anthu omwe anali ku ma dansiwa ndipo anayamba kumuwowoza oyimbayu. Ena anayamba kumugenda ndi ma botolo a mowa ndipo oyimbayu sanayimbenso koma anachoka pa siteji chothawa.

Lero, Onesimus wapepesa ndipo wanena kuti sadzayimbaranso zomanyoza anthu chomwechi.

“Sindimayenera kuyankhula choncho potengera mavuto omwe anthu akukumana nawo. Ndikudziwa kuti zonse ndi za chabe koma ndi chikondi chomwe chimapangitsa chibwenzi kulimba,” watero woyimbayu mu uthenga wake.

 

Follow us on Twitter:

 

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.