A Malawi akhazula Med C

Advertisement

A Malawi ang’alura katswiri oyimba nyimbo zamakono Medson Kapeni amene amadziwika kuti Med C, kamba kakhalidwe lomwe waonesa kuti asiyane ndi kampani ya Magic Fingers LL yomwe imamuthandiza.

Malingana ndi malipoti, mnyamata yu sadapite kojambula kanema wa imodzi mwa nyimbo zake, ngakhale kampaniyi idali itakonza madongosolo onse oyenelera.

Komanso malipoti wa akuti katswiri yu adali ndi khalidwe lo pemphapempha makobiri ku kampaniyi zomwe zidapangisa akuluakulu a kampaniyi kuti achose chidwi chawo pa iye.

Izi zadzesa mkwiyo pakati pa A Malawi. Ambiri akukhulupilira kuti oyimbayu waonesa mtima osayamika.

“Akuyenera alandire chipulumuso mwanayu, mkutheka ena ake adamuloza. Munthu oganiza sangapange izi,” atero A Lilian Mhango mu Ndemanga yawo

A Nancy Zimpita nawo athilira ndemanga motere: “Iyi ndi misala iyi, anthu sangamakupase mwai iwe kulephera kuugwirisa ntchito. Ndi pemphero langa kuti ambuye amuyendere.”

Ngakhale anthu amukhazula Med C, ena amuyamikira kamba kovomereza za khalidwe lake.

“Chomwe chandikondweresa pa nkhani ya Med C ndichoti sanabise chilungamo, akanakhala wina akanazibakira. Angositha khalidwelo basi,” Atero Tha Kwez

Med C adayamba kuthandizidwa ndi kampani yi chaka chatha. Mgwirizano wawo udali wa zaka ziwiri ndipo udali wa ndalama zokwanira K10 million.

Magic Fingers LL yomwe m’modzi mwa eni ake ndiTionge Mhango, idatenga mnyamatayu atasiya kuthandizidwa ndi Patience Namadingo.

Follow us on Twitter:

Advertisement

2 Comments

  1. Koma mupeze munthu wolemba Chichewa chabwino, else mukanangotipatsira nkhaniyi m’Chingerezi!

    1. Nkhani kungoilemba chinyasalande basi poti owelenga ndi ma nyasaso basi potozeni potozeni zosaveka shame on you

Comments are closed.