Bwalo la ndege la Chileka ligwetsedwa mwezi wa mawa

Advertisement

Bwalo la ndege la Chileka ligwetsedwa mwezi wa mawa kuti pamangidwe lina latsopano.

Nduna yoona zamtengatenga Jacob Hara yatsimikiza kuti ntchito yogwetsa bwaloli iyamba mwezi wa mawa.

Iwo anati chifukwa chakuti bwaloli lakhalitsa, sipakufunikanso kungolikonza mwa apo ndi apo koma kuligwetsa lonse nkumanga lina latsopano ndipo ntchitoyi ichitika ndi kampani ina yaku Japan yomwe yayamba kale kuunikira m’mene ntchito iyendere pamalopa.

Dziko la Japan lalonjeza kuthandiza dziko lino ndi katundu monga zipangizo zamakono zomwe mwa zina ndi zothandizira anthu olumala kuti aziyenda mosavutika pamene ali kubwalo la ndegeli zomwe zonse akaziphatikiza zikuyembekezera kukwana ndalama zopitikira K2billion.

Malingana ndi a Hara, ntchito yomanganso bwaloli ikuyenera kuzatha mu chaka cha 2025.

Boma mu chaka cha 2019 linakonza komanso kukunza misewu yoyenda ndege ntchito yomwe inkayenera kugwirika miyezi itatu ndipo panthawiyi ndege zing’onong’ono zokha ndi zimene zimaloredwa kufika pa bwaloli pomwe zikuluzikulu zimafikira ku bwalo la ndege la Kamuzu  mzinda wa Lilongwe.

Follow us on Twitter:

Advertisement