‘Afana otani?’ a Chilima, a Chimwendo, a Matemba ndi ena awatchula pa mndandanda wa okudya za Sattar

Advertisement

Kuganiza bwino ankanena wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino ndikutheka si pa ndale pokha, mwinanso kuchenjela manja kumene.

Malipoti ochokela mu dziko la United Kingdom asonyeza kuti a Saulos Chilima ali pa mndandanda wa anthu amene akukayikilidwa kuti akhala akulandila ziphuphu kwa mkulu okayikilidwa za katangale a Zuneth Sattar.

Malinga ndi malipoti amene anayalidwa mu khoti ku UK uko, a Sattar ati ali ndi ma ubale ochuluka mu boma la Malawi. Ambili mwa maubale amenewa akuoneka kuti anawapanga kudzela mu katangale.

Mwa anthu ena amene atchulidwa kuti ali mu goli la katangale la a Sattar ndi a Chilima kudzanzo mkulu wa a polisi a George Kainja. Kupatulapo awiliwa, mkulu wa zachinyamata mu chipani cholamula cha MCP amenenso anakhalapo nduna yoona za chitetezo a Richard Chimwendo Banda nawo akuganizilidwa kuti ndi kamberembere amene wadya nawo za a Sattar.

Nawo a Reyneck Matemba amene adapachika a Thomson Mpinganjira kamba kofuna kuchita ziphuphu atchulidwa pa mndandanda umenewu. A Matemba anali mkulu wa kale wa bungwe lothetsa ziphuphu. Iwo si katswiri wa za malamulo yekha amene watchulidwa, nawonso a John Suzi Banda amene anakhalapo mtsogoleri wa bungwe la ma loya atchulidwa mu bwalo la ku Mangalande kuti akukhala ngati anadyapo.

Mndandanda uwu umene uli ndi anthu ambili kuposa amene atchulidwa kale wafikanso kunyumba ya chifumu ndipo mkulu woyang’anila nyumba izi a Prince Kapondamgaga nawo atchulidwa kuti akukhala ngati amatenga nzeru kwa Sattar kuti nawo apatsidwe ndalama.

Malinga ndi malipoti, a Sattar akhala akulipilila sukulu ana a anthu oweluza milandu mu ma bwalo a mu dziko lino.

Zikuyembekezeleka kuti a Sattar akayamba kuwazenga mlandu ku Buliteni, anthu ambili aululika kuyambila mu boma la a Mutharika kufikila la a Chakwera.

Advertisement