Ophunzira 3 million salemba mayeso ku Sri Lanka, boma likukanika kugula mapepala

Advertisement

Olemba: Gracious Zinazi

Dziko la Sri Lanka lomwe linachita malire ndi dziko la India latsimikiza kuti ana a sukulu pafupifupi 3 million salemba mayeso chifukwa dzikoli likukumana ndi mavuto a zachuma ndipo silingakwanitse kugula mapepala.

Boma la dzikoli lilibe ndalama zosindikizira komanso kugulira mapepala opangira mayeso chifukwa chakusowa kwa ndalama zakunja maka mu mzinda waukulu wa dzikoli otchedwa Colombo pachifukwa ichi ndikovuta kuitanitsa mapepala kuchokera ku maiko ena.

Akuluakulu azamaphunziro ati mayeso akumapeto kwa telemu omwe amayembekezereka kuyamba lero lolemba, azalembedwa mtsogolomu chifukwa chakusowa kwa mapepala pomwe dzikoli lili pa nkhondo yazachuma yomwe sinayambe yakhalapo kuchokera pomwe analandira ufulu 1948.

“Akuluakulu ama sukulu osiyanasiyana sakwanitsa kulembetsa mayeso chifukwa osindikiza mayeso alibe ndalama zakunja zomwe zimathandizira kugulira mapepala komanso inki kuchokera ku maiko ena,” dipatimenti ya maphunziro ku Western Province inatero.

Monga maiko ambiri amachitira pamaphunziro, ku Sri Lanka nakonso mayeso akumapeto kwa telemu iliyonse ndiomwe amathandizira kudziwa ngati mwana wa school ali oyenera kukalowa kalasi ina kapena ayi kumapeto kwa chaka.

Malingana ndi uthenga ochoka ku boma la dzikoli, ophunzira pafupipafupi 3 million salembanso mayeso awo akumapeto kwa telemu.

International Monetary Fund (IMF) lachisanu lapitari yaonetsa chidwi chofuna kukomana ndi mtsogoleri wadzikoli Gobataya Rajapaksa lachitatu likubwerali ndicholinga chofuna kuzakambirana momwe angalithandizire dzikoli kuchoka mu msapha wangongole omwe unazetsa kuchepa kwa ndalama zakunja zolowa mdzikoli.

Kumayambiriro kwa chaka chino, dziko la Sri Lanka linapempha dziko la China lomwenso limalithandiza kwambiri pa chuma kuti alithandize kuchoka mu msampha wa ngongole zakunja omwe ukuzetsa mavuto akusowa kwa chakudya, mafuta agalimoto komanso mankhwala mzipatala, koma mpaka pano palibe yankho logwirika kuchoka ku boma la China.

Advertisement

One Comment

Comments are closed.