Makampani opanga mafuta ophikira atsitsa mitengo ya mafuta mwezi wamawa

Advertisement

Boma la Malawi kudzera ku unduna wa zamalonda lati makampani onse opanga komaso kugulitsa mafuta ophikira mdziko muno avomera kuti atsitsa mitengo kuyambira pa 1 mwezi wamawa.

Izi zadziwika potsatira mkumano omwe boma linapangitsa sabata ino ndi makampani onse opanga komaso kugulitsa mafuta ophikira komwe mbali zonse zokhudzidwa zimagwirizana pa zoyenera kuchita pankhani yofuna kutsitsa mitengo.

Malingana ndichikalata chomwe unduna wa zamalonda watulutsa Lachinayi pa 17 March, boma lalamura kuti makampani onse ogulitsa mafuta ophikira atsitse mitengo potsatira kuchotsedwa kwa nsonkho wina pamafuta ophikirawa.

Chikalatachi chati mbali zonse zagwilizana kuti boma likangotulutsa chikalata chotsimikiza za kuchotsedwa kwa nsonkhowu, kampani iliyose yopanga komaso kugulitsa mafuta ophikira idzayenera kulemba kalata kufotokoza za mapelesenti omwe yatsitsira mitengo yamafutawa.

“Makampani onse atsimikizira boma za kudzipeleka kwawo pa nkhani yotsitsa mitengo yamafuta ophikira ndi cholinga choti anthu ogwilitsa ntchito mafutawa apindule ndikuchotsedwa kwa nsonkho ndipo izi zikuenera kuchitika kuyambira pa 1 April, 2022, boma likatulutsa zikalata zoyenera pankhaniyi,” yatelo kalata yochokera ku unduna wa zamalonda.

Mumchikalatachi, undunawu watiso mafuta ophikira akapitilirabe kukwera mitengo panthawi yanenedwayi, boma la Malawi pofuna kuonetsetsa kuti mitengoyi yatsikabe basi, lidzalora makampani ena kuti nawo ayambe kubweletsa mafuta awo mdziko.

Undunawu watiso boma liwonetsetsa kuti zipangizo zopangira mafuta ophikira zomwe zimachoka maiko akunja zisamasowe mdziko muno komaso lati lionetsetsa kuti alimi asoya mdziko muno azigulitsa mbewu zawo pamitengo yokwera ngati njira yowalimbikitsa kuti asasiye kulima mbewuyi.

Potsiliza boma lati liwonetsetsaso kuti mbali zonse zokhudzidwa pankhaniyi zizikumana pafupipafupi ndi cholinga choti zidzitha kukambirana njira zothetsera mavuto pankhani ya mafuta ophikira.

Pakadali pano, botolo la 2 litazi la mafuta ophikira likugulitsidwa pa mtengo osachepela K6000 pamene chigubu cha 5 litazi chikugulitsidwa pamtengo osachepela K13000 zomwe zakhala zikudandaulitsa a Malawi ambiri.

Advertisement