Madotolo adandaula ndi kuchuluka kwa mankhwala a zitsamba pamsika

Advertisement
African-medicine

Gulu la madotolo mdziko muno la Society of Medical Doctors (SMD) ladandaula ndi kuchuluka kwa mankhwala a zitsamba m’misika ya mdziko muno zomwe lati zikukolezera matenda ena pakati pa anthu.

Izi ndi malingana ndi mtsogoleri wa gulu SMD Dr Victor Mithi omwe amayankhula ndi imodzi mwa nyumba zofalitsira mawu mdziko muno ndipo anati izi zikusokoneza ntchito yolimbana ndi matenda ena.
A Mithi ati ndizokhumudwitsa kwambiri kuti misika yambiri mdziko muno yadzadza ndi mankhwala azitsamba omwe eniake ogulitsa omwe ndikuphatikizapo asing’anga, akumati amachilitsa matenda osiyanasiyana.

Iwo ati kupezeka kwa mankhwalawa mmisika ya mdziko muno zikupangitsa kuti chiwerengero cha anthu omwe akumapezeka ndi matenda okhudza ipso komaso chiwindi achuluke kwambiri.
Mkuluyu anatiso kuopsa kwa mankhwalawa ndi koti samakhala ndi mulingo weniweni kwa munthu yemwe akuwagwiritsa ntchito komaso ati ambiri mwa mankhwalawa amakhala osayezedwa ngati ali abwino ku miyoyo ya anthu.
“Ifeyo ngati SMD tawona kuti mchitidwe agulitsa komaso kuitanira mankhwala azitsamba ukuchuluka kwambiri. Mukapita mzipatalamu mukapeza kuti anthu akubwera koma ipso zawo zowonongeka kwambiri komaso chiwindi chawo chasiya kugwira ntchito.
“Izizi zimabwera kwambiri kaamba komwa mankhwala a zitsamba amene ambiri akumakhala kuti sanayezedwe komaso sanaunikidwe bwino bwino ngati ali othandizadi ku matupi a anthu,” atelo a Mithi.

Pakadali pano a Mithi ati pakufunika malamulo amene aziletsa mankhwala a zitsamba omwe sanayezedwe kupezeka pamsika ndi cholinga choti zina mwa nthenda zomwe mankhwalawa akolezera, zichepe.

Advertisement