A ndale awapempha kuti azigwira bwino ntchito ndi achinyamata

Advertisement

Wolemba: Sopani Ng’ambi

Wachiwiri kwa mfumu ya mzinda wa Mzuzu, a Tony Gradwell Mwenitete, wapempha zipani za ndale m’dziko muno kuti zizigwira bwino ntchito ndi achinyamata powaphunzitsa makhalidwe oyenera omwe angawathandizire kukhala nzika zodalirika.

Iwo adanena izi pa mwambo womwe achinyamata a chipani cha Malawi Congress Party ochokera m’mzinda wa Mzuzu amapereka katundu osiyanasiyana monga ufa ophikira ku gulu la anthu okalamba lotchedwa Wamzako ndi Wako Yemwe Organization, lolemba m’muzindawu.

“Ndizokhumudwitsa kumva kuti zipani zina zimagwiritsa ntchito achinyamata ngati zida zokolezera ziwawa. Nthawi yakwana yoti tiyambe kuwaphunzitsa makhalidwe oyenera achinyamatawa kuti akhale nzika zodalirika,” a Mwenitete adatero.

Mfumuyi kotero idayamika achinyamata omwe anapereka thandizoli ndipo idapemphanso achinyamata a zipani zina ndi mabungwe ena kuti atengelepo phunziro.

“Ena nawonso ayenera kuti azitero. Achinyamata alimo ambiri m’dziko muno ndipo ngati aliyense angakhale ndi mtima ngati uwu, ndiye kuti dziko lipita patsogolo,” idatero mfumuyi.

M’modzi mwa achinyamata a gululi, a Gideon Gondwe, anati iwo anasankha kugwiritsa ntchito tsiku lomwe anthu amawonetsa chikondi kwa okondedwa awo, la Valentine’s Day, kuti nawonso awonese chikondi chawo kwa anthu a achikulirewa.

A Gondwe anatinso anaona kuti anthu ambiri achikulire amakumana ndi mavuto osiyanasiyana pamoyo wawo wa tsiku ndi tsiku choncho kuwapatsa katundu monga chakudya ndi chinthu cha mtengo wapatali.

“Awa ndiwo anatilera, amatilangiza komanso ndiwo amasunga mbiri ya dziko lino, choncho sibwino kuti azivutika ana awo tilipo – kutengaranso kuti ambiri mwa iwo sagwira ntchito,” adatero a Gondwe.

Naye m’modzi mwa akuluakulu a gulu la Wamzako ndi Wako Yemwe Organisation, a Jalex Tembo, anathokoza achinyamatawa ponena kuti thandizoli labwera m’nthawi yake.

“Ndife okondwa kwambiri kamba ka thandizoli chifukwa lafika mu nthawi yake, ndipo apapa atithandiza kwambiri,” adatero a Tembo.

A Tembo adawonjezera popempha anthu ena omwe ali ndi kuthekera kothandiza anthu osowa kuti athe kutero.

Wina mwa katundu yemwe achinyamatawa anapereka ndi monga mafuta ophikira, ufa ophikira, chuga komanso mchere.

Advertisement