Mbava yaba mfuti, zipolopolo ku polisi

Advertisement

Zina ukamva kamba anga mwala. apolisi ku Zomba akusakasaka mbava yomwe yaba mfuti, zipolopolo khumi komaso ma foni a m ’manja awiri mu ofesi ya apolisi.

Malipoti akusonyeza kuti nkhaniyi yomwe yadulitsa mitu yazizwa, yachitika cha mma 5 kololoko m’mawa wa lolemba pa 14 February, 2022 ku ofesi ya polisi ya Zomba.

Zikuveka kuti mbava yolimba mtimayi inathyola ofesi ya polisiyi ndipo italowa mkati inalunjika pa kauntala ndikutenga mfuti imodzi, zipolopolo khumi (10) komaso inazula patchaja mafoni awiri omwe ndi a apolisi omwe amagwira ntchito pa nthawiyi.

Malipoti ena osatsimikizika akuti wa polisi mmodzi yemwe amagwira ntchito pa nthawiyi, anaona dzanja likulowetsedwa mukauntala ndikunyamula mfutiyo koma pamene iye anakuwa kuti athandizidwe, mbavayi inali itaonetsa kale phanzi, kuthawa.

Atafusidwa ndi nyumba zina zofalitsira mawu mdziko muno, mneneri wa polisi ya Zomba a Sub Inspector Patricia Supliano komaso mneneri wa apolisi mdziko muno a James Kadadzera, sanakane kapena kuvomera za nkhaniyi.

Koma ngakhale akuluakuluwa alephera kufotokoza tsatane tsatane wankhaniyi, zikuveka kuti apolisi awiri omwe amagwira ntchito pa nthawiyi, anatsekeledwa mumchitolokosi ndi apolisi amzawo.

Pakadali pano, nkhaniyi yapeleka mantha pakati pa anthu mdziko muno kaamba koti anthu ambiri akuzifusa kuti ngati mbava zikukwanitsa kukaba ku polisi, kuli bwanji malo ena omwe ndi a munthu wamba?

Advertisement