Auzeni atulutsiretu manyaka a nyimbo zawo chifukwa ndikudza mwaukali – Onesimus

Advertisement

Katswiri oyimba nyimbo za uzimu Onesimus wachechenjeza oyimba anzake kuti atulutsiretu nyimbo zawo zolumpha moto zo, iyeyo asadadze ndiukali.

Bambo Onesimus anena izi pamene amadziwisa mtundu wa Amalawi kuti atulutsa nyimbo yomwe itagwedeze dzikoli.

“Auzeni atulutsiretu nyimbo zawozo, chifukwa mkadzatulutsa yanga ndizaanyenyanyenya onsewa,” atero Onesimus

Iwowa anena izi pamene oyimba ambiri mu dziko lino alengeza kuti akufuna atulutse nyimbo zawo. Ena mwa oyimbawa ndi Patience Namadingo amene amakhala mu dziko la Zambia komanso Gwamba.

Namadingo akutulutsa nyimbo yake yomwe sadaitchule pa 11 February, pamene Gwamba watulutsa nyimbo yake yotchedwa Lipenga, yomwe waimba ndi Quest, dzulo usiku.

Kulankhula kwa Onesimus amene dzina lake lobadwira ali Armstrong kalua, kwapangisa Amalawi ena kunena kuti mkuluyu wayamba matama.

Koma poyankha pankhaniyi, Kalua wakana akuti sakupanga matama. Iyeyo walangiza anthu kuti azisiyanisa kuzikhulupilira ndikupanga matama.

 

 

Advertisement