Yambani kupeleka ndalama ku mpira kuti tithane ndi misala – nduna yauza a Escom

Advertisement

Pamene dziko lino lili pa mpanipani kusaka ndalama loti ntchito za magetsi zikhale zolongosoka, nduna yatsopano yoona za mphamvu za magetsi a Ibrahim Matola wauza bungwe la Escom kuti liyambilenso kupeleka ndalama kwa matimu a mpira ati ndi cholinga chothana ndi matenda a mu ubongo.

Polankhula pamene anakumana ndi ogwila ntchito ku bungweli limene lakhala likudandaula za chuma, a Matola anati bungwe la Escom likuyenela kuyambilanso kupeleka ndalama ku matimu a mpira ndi cholinga choti likonze mbili yake komanso kuti athandizane ndi boma pothana ndi matenda a mu ubongo.

Aka kanali koyamba a Matola kukumana ndi akuluakulu a bungwe la Escom Sabata latha, a Matola anakayendela ku Nkula kumene kwaonongeka koopsa ndi mvula ya mkuntho ya Ana yomwe inaumbudza dziko lino sabata zapitazi.

Koma powayankha a Matola, mkulu wa bungwe la Escoma Clement Kanyama anati nkhani imene anabweletsa a Matola akaipeleka ku bodi yaikulu ya Escom.

Bungwe la Escomlakhala likudandaula kuti lili pa mavuto a zachuma. Kumayambililo kwa chaka chino, bungweli linanena kuti ndondomeko zoti anthu azilumikiza magetsi mwa ulele zakhala zikukanika kamba ka mavuto a chuma.

A Matola asankhidwa ndi a Chakwera sabata latha ndipo alowa m’malo mwa a Newton Kambala amene anachotsedwa ntchito kamba kokhudzidwa ndi nkhani za katangale.

Advertisement