A Mpinganjira atuluka kundende pa belo

Advertisement

Mpondamatiki Thom Mpinganjira tsopano akupuma mpweya wabwino bwalo la milandu la apilu litalamula kuti atuluke ku ndende pa belo.

A Mpinganjira analamulidwa kukakhala ku ndende kwa zaka zisanu ndi zinayi (9) kaamba kowaganizira kuti ankafuna kupeleka ziphuphu kwa oweruza milandu omwe amayendetsa mlandu wa chisankho chaka cha 2019.

Koma ataseweza jele kwa miyezi itatu yokha, bwalo la milandu la apilu mumzinda wa Blantyre kudzera kwa oweruza milandu Frank Kapanda, lalamula kuti khumutchayu atuluke ku ndende ya Chichiri komwe amaseweza.

Malingana ndi a Alexious Nampota omwe akuimilira a Mpinganjira, oweruza milanduyu wapeleka chigamulo chowatulutsa a Mpinganjira pa belo pofuna kuwapatsa mpata kuti akamang’ale ku khothi la apilu pachigamulo chomwe analandira pamlandu wawo.

A Nampota ati bwalo la milandu lapeleka chigamulochi kaamba koti a Mpinganjira akhala akudandaula kuti sakupeza bwino mthupi ndipo oweruza milandu Kapanda anati ndikuphwanya malamulo kuwasunga a Mpinganjira ku ndende akudwala.

Iwo ati bwalo lamilanduli lapezaso kuti yemwe anaweruza mlandu wa mpondamatikuyu a Dorothy De Gabrielle analakwitsa zinthu zina makamaka posapeleka mpata kuti a Mpinganjira alandile chilango choyenera.

‘’Anthu ambiri akuvomeleza kuti chilungamo chitha kuoneka bwino bwino ngati a Mpinganjira atakhala kaye kunja kwa ndende podikira kuti akachite apilu pachigamulo chomwe anapatsidwa.

“Oweruza milandu waona kuti kuika munthu ku ndende yemwe sakupeza bwino mthupi komaso yemwe nkhani yake akufuna itavedwaso ndikumulakwira oganizilidwayo,” atelo a Nampota.

A Nampota anaonjezeraso kuti munthu amene ndiosalakwa akakakhala ku ndende tsiku limodzi, zimapeleka chisonyezo choti china chake sichikuyenda bwino pankhani yokhudza chilungamo.

Advertisement

One Comment

  1. Ingonenani kuti mwamunkhululukira osat zodwalazo Kuli ma kaidi ambirimbiri akudwala Ku ndende naonso muwatulutsa hahaha

Comments are closed.