Mulandira malipiro anu mochedwerako, atero akuluakulu a ADMARC

Advertisement
Admarc

Bungwe la Agriculture Development and Marketing Corporation (ADMARC) lalemba kalata kuwuza anthu ogwira ntchito ku bungweli kuti adekhe kaamba kakuti mwezi uno alandira malipiro awo mochedwerako chifukwa cha mavuto azachuma omwe akuta bungweli.

Malingana ndi a Ethel Zilirakhasu omwe ndi mkulu owona za anthu ogwira ntchito ku bungweri ati chuma sichikuyenda bwino ku bungweli koma apempha anthu kuti adekhe chifukwa akulu akulu akuyesa njira iliyonse kuti anthu alandire malipiro awo a mwezi wa Januwale.

Koma pakulankhula ndi Malawi24, kuzera pa lamya m’modzi ogwira ntchito ku ADMARC yemwe anatipempha kuti tisamutchule dzina lake wati zinthu sizikuyenda bwino ku bungweri kupatula kuchedwa kulandila ndalama kulinso mavuto ankhani nkhani omwe akudza kamba kosowekera utsogoleri wa luntha.

Iwo anapitiliza kuti kuchedwa kulandila malipiloku kwawakhudza zedi moti pakadali pano angongole akuwavutitsa kufuna ndalama zawo.

ADMARC ndi bungwe la boma loyima palokha lomwe linakhadzikitsidwa mu chaka cha 1971 ndicholinga chotukula alimi komanso chuma cha dziko koma pakutha kwa nthawi zinasinthidwa kuti bungweri lisayike mtima pa phindu koma kuwonetsetsa kuti chakudya chilipo chokwanira mdziko muno.

Advertisement