Sitikudziwa kuti musiya kukhala mu mdima liti – yatelo EGENCO

Advertisement

Kampani yopanga magetsi mdziko muno ya Electricity Generation Company (EGENCO) yati siikudziwa kuti vuto lakuzimazima kwa magetsi, lomwe layamba kaamba ka mvula yamphamvu, litha liti.

Nkhaniyi ikutsatira kuzimitsidwa kwa makina m ’malo ena opangira magetsi lolemba pa 24 January kaamba ka mvula ya mphamvu yomwe mmadera ambiri mdziko muno zomwe zapangitsa kuti mitsinje yochuluka kuphatikizapo Shire ikhale yosefukira.

Malingana ndi akuluakulu a EGENCO, makina ena kumalo opangira magetsi a Kapichira komaso Tedzani IV anazimitsidwa kaamba koti anali pachiopsezo choti anakatha kuonongeka potsatira kusefukila kwa madzi komwe kwachitika kumayambiliro kwa sabata ino.

Ku Kapichira mvula yaononga malo opangira maetsi

EGENCO yati kuyambira pomwe makinawa anazimitsidwa lolemba, ogwira ntchito ku kampaniyi akhala ali kalikiliki kuti makina onse omwe anasiya kugwira ntchito abwelere nchimake.

Koma ngakhale zili choncho, kampaniyi kudzera mumchikalata chomwe yatulutsa lachitatu yati ngakhale ntchito yobwezeretsa makinawa yatsala pang’ono kutha, koma siikudziwa kuti kuthima thima kwa magetsi mmadera ochuluka mdziko muno kutha liti.

“Mmene imati 11:00 mmawa pa 26 January, tinali ndimphanvu za magetsi ochokera ku madzi zokwana 152.45 MW, 14.53MW kuchokera ku majeneleta komaso 1.3MW kuchokera ku mphavu ya dzuwa, zonse pamodzi zinali 168.28MW koma timakwanitsa kugawa 109.40MW.

“Mwatsoka, sitinganeneretu tsiku lenileni lomwe magetsi ayambe kugawidwa bwino bwino ngati kale koma ndi thandizo lochokera ku boma titha kuwatsimikizira anthu kuti tikuyesetsa kuti maina onse ayambileso kugwira ntchito,” yatelo EGENCO.

Pa nkhani yomweyi, nalo bungwe logulitsa magetsi la Electricity Supply Corporation of Malawi (ESCOM) ladandaula kuti ntchito yogulitsa magetsi ikuvuta kaamba koti nthambo za magetsi zochuluka zawonongeka mmadera ambiri.

ESCOM yati pakadali pano nayo ikupanga zothekera kuti ikoze nthambo zonse zomwe zaonongeka kaamba ka mvula yamphanvu yomwe inagwa kwa masiku awiri osalekeza m ’madera ambiri mdziko muno makamaka a mchigawo chakummwera.

Advertisement