Moto wawotcha wailesi yakanema ya Luntha

Advertisement

Moto wawotcha ofesi yowulutsilako mawu ndi zinthunzi ya kanema wa Luntha ku Lilongwe.

Malingana ndi uthenga omwe akulu akulu ku wailesiyi atulutsa ati padakali pano sakudziwa chomwe chinayambitsa motowu.

Iwo apitiliza kunena kuti motowu wawononga zinthu monga zojambulila, zotchinjila mawu kuti azimveka bwino komanso zomwe zimabweletsa mphepo yabwino mu ofesi mwawo.

Kucha kwa lero anthu omwe amatsatira kanemayu anali odabwa kuti samatha kuwonela mapemphero monga momwe zimakhalila nthawi zonse.

 

 

 

Advertisement