Mabungwe akana mchitidwe obaya katemera mokakamiza

Advertisement

Bungwe la Centre for Democracy and Economic Development Initiatives (CDEDI) lati likukhulupilira kuti a Malawi ali ndi ufulu wosankha kubayitsa kapena kusabayitsa katemera ndipo kubayitsa katemerayu kusakhale kokakamiza.

Nkhawa ya bungwe la CDEDI ikubwera pomwe boma la Tonse motsogozedwa ndi mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera anena kuti ayamba kupereka katemera okakamiza kuyambira mu January, 2022.

Poyankhula pa nkumano wa a tolankhani lachiwiri ku Lilongwe, Mtsogoleri wa  Bungweli Sylvester Namiwa anaonetsa kukhumudwa ndi zomwe Boma lalengeza kuti katemera wa Kolona akhala wokakamiza kwa anthu ogwira ntchito za boma monga aphunzitsi.

Iwo anati ku CDEDI akudabwa ndi ganizo la bomali poganizira kuti mayiko omwe ali ndi chiwerengero cha anthu obayitsa katemera wa Kolona ambiri monga Israel, United Kingdom (UK) ndi mayiko onse aku ulaya komwe kuli anthu ambiri omwe apezeka ndi matenda a Kolona sanapange katemera wa Kolona kukhala wokakamiza.

Namiwa adawonjezera pofunsa kuti cholinga cha boma la Malawi kupanga katemera wa Kolona kukhala wokakamiza ndi chani chifukwa pakadali pano, palibe umboni ogwirika wakuti katemera owonjezera akufunika kapena ndi waphindu.

“Koma zikuwoneka kuti akumapereka chiwopysezo chifukwa palibe kafukufuku wambiri wosonyeza kuyipa kwake. Tikukhulupilira kuti a Malawi tiphunzire kukhala ndi Kolona monga takhala tikuchitira ndi matenda ena amene akhala akutivutitsa.

“Nkhondo ya Kolona isatiyawalitse kuti tikulimbana ndi matenda ena monga a malungo, HIV komanso EDZI, Khansa, TB, BP, kunyentchera komanso umphawi wadzaoneni womwe ukusautsa a Malawi ambiri.  Tikupepha boma la Tonse kuti liphunzire kupewa kumangotsanzira zomwe zikuchitika kumayiko ena, mwachitsanzo kulamula anthu kuti apite pa m’bindikiro ndi njira zina zokakamiza popanda zifukwa zomveka bwino,” iwo anatero.

Mkulu wa CDEDI anati m’malo mokakamiza anthu kuti abayitse katemerayu, boma lilimbikitse mkhalidwe wa nthanzi monga kulimbikitsa anthu kuti azidya mosamalitsa, ndikuti azipewa zakudya zomwe zikuyika moyo wawo pa chiwopysezo chamatenda osapatsirana.

Namiwa adatinso Bungwe la CDEDI likukhulupilira kuti a Malawi ali ndi ufulu wosankha kubayitsa kapena kusabayitsa katemera ndipo kubayitsa katemerayu kusakhale mokakamiza.

“A Malawi akuyenera kudziwa kuti kuli ziwonetsero zamkwiyo zosatha ku mayiko monga a Australia, UK ndi Amelika zotsutsana ndi kukakamizana katemera. Anthu ambiri sakutha kuyankhula momasuka pa nkhani ya Kolona mumasamba amchezo chifukwa chowopa kuchotsedwa ntchito, komanso kaamba kakuti nkhani zokhudza Kolona zimatsatidwa kwambiri ndi masamba a mchezo monga Twitter komanso Facebook. Izi zikumapereka mafunso kwa anthu ambiri kuti nkhaniyi ndi ya Kolona kapena zina zake?” Namiwa adawonjezera

Pakali pano, iwo anapempha mabwalo a milandu kuti ayimitse katemera wokakamiza wa Kolona kwa katemerayu sikunatsimikizike.

 

 

 

Advertisement