A Chakwera sangangolamula kuti mafuta atsike – Nundwe

Advertisement

Anthu osamvetsetsa za chuma ndi amene ali ndi phuma kuti mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera atsitse zinthu, watelo mkulu wa asilikali lero ku Salima.

A Nundwe amene amayankhula pa mwambo omwe asilikali atsopano amalandilidwa kuti amaliza maphunzilo awo ananena kuti anthu ena akulephela kumvetsa m’mene chuma cha dziko chimayendela.

“Tili mu free market economy,” iwo anatelo, “President sangangolamula kuti tsitsani mafuta lero…”

Iwo anaonjezelapo kunena kuti kuli anthu ena akufalitsa bodza lokhudzana ndi asilikali kumati sakukondwa.

“Ife tikakhala ndi mavuto timakakumana ndi mtsogoleri kumuuza, sitingapange zionetselo iyayi,” anatelo a Nundwe.

Iwo amayankhula izi pamene malipoti atchuka oti anthu ena azachitetezo sali okondwa ndi ulamulilo wa a Nundwe, komanso ena anati sakukondwa ndi malipilo awo ngakhale nthawi yolandila malipiloyo.

A Nundwe anapezelaponso mwayi wina odzudzula anthu ogwila nawo ntchito kunena kuti asiye kusaka ma udindo kuchokela kwa a ndale. Iwo anati a ku nyumba ya boma akhala akulembelapo kalata akuluakulu aku usilikali kuti akweze anthu ena pa udindo.

“Pena umangolandila kalata kuchoka ku nyumba yachifumu kumva kuti uyu mumukweze pa udindo. Izi si zoona,” iwo anatelo.

Advertisement

One Comment

  1. You see how people who got positions through political push. This is an Army Commander and decides to comment on politics and yet he is the same person who was against that on the involvement of the army in politics. This is very clear that he is a soldier-turned politician. My advice is that he should just keep quiet and never to comment on such things because thats not part of his role. Army Commander sir, just zip your mouth.

Comments are closed.