Blantyre Water Board ikufuna kukwezaso mtengo wa madzi chaka cha mawa

Advertisement

Anthu okhala mu mzinda wa Blantyre ayembekezere kuti chaka cha mawa mtengo wa madzi utha kukweraso kaamba koti bungwe logulitsa madzi la Blantyre Water Board (BWB) lati likufuna kupempha boma kuti likwezeso mtengo wa madziwu ndi K40 pa K100 iliyonse.

Izi zadziwika pamkumano omwe bungweli linali nawo sabata ino mumzinda wa Blantyre komwe mwazina limakhazikitsa ndondomeko ya ntchito zomwe bungweli likufuna kuchita zaka zisanu zikubwerazi.

Malingana ndi mkulu oyang’anira za zachuma ku Blantyre Water Board a Paul Chiumia, mtengo wamadzi omwe ukugwira ntchito pano siukugwirizana ndi ndalama zomwe bungweli limaononga kuti madzi akafikile makasitomala.

“Vuto lina ndi mitengo yomwe timagulitsira madziwa,. Mitengoyi ndiyotsika kwambiri poyelekeza ndi ndalama zomwe timalowetsa tikamawanga madzi wa kuti akafikile makasitomala ali abwino,” watelo Chiumia.

A Chiumia anati akufuna kupempha kwa adindo kuti chaka chamawa mitengo yogulitsira madziwa idzakwere ndi K40 pa K100 iliyonse komaso kuti muchaka cha 2023 mitengoyi idzakwere ndi K10 pa K100 iliyonse.

Apa mkuluyu anati kukwezaku kuzathandizira kuti bungweli lizizakwanitsa kupanga phindu pantchito yogulitsa madzi zomwe ati zitha kuthandizira kuti ntchito yogulitsa madzi idziyenda bwino.

Pamkumano omwewu zadziwikaso kuti bungwe la Blantyre Water Board limapeza ndalama zokwana K1.5 billion pachaka koma lati pa ndalamayi, K1.2 billion imapita kubungwe logulitsa magetsi la ESCOM zomwe akuti mzodandaulitsa kwambiri.

Pakadali pano bungweli lapempha boma kuti lilithandize kubweza ngongole yokwana K24 billion yomwe ili nayo ndibungwe la ESCOM pa ma getsi omwe bungweli lakhala likugwilitsa ntchito mmbuyomu.

Nkhani yofuna kukweza mtengoyi ikubwera pomwe posachedwapa bungweli lakweza mtengo ogulitsira madzi ndi K40 pa K100 iliyonse zomwe anthu anadandaula kale kuti kukwezaku kunali kwakukulu kwambiri

Advertisement