Amalawi, pemphelani kosalekeza – watelo Mutharika

Advertisement

Mu buku la Mafumu mu Baibulo ati muli nkhani ya Eliya, amene anapemphela ataona ng’amba. Mtsogoleri opuma wa dziko lino a Peter Mutharika ati a Malawi akuyenela kuchita monga anachitila Eliya: kugwada mozichepsa pa maso pa Chauta.

A Mutharika ati kusowa kwa mvula mu dziko lino tsopano kwafika poopsa ndipo a Malawi onse ayenela apinde maondo kuthila pemphelo. Malinga ndi chikalata chimene atulutsa a Mutharika, Malawi akudutsa mu nyengo zoopsa.

Iwo ati kusowa kwa mvula mu dziko muno kwafika poopseza umoyo wa a Malawi.

“Mneneri Eliya mu Baibulo atakumana ndi vuto lotele, anapemphela,” watelo Mutharika.

“Ngakhale makolo athu kalelo amakathila nsembe akakumana ndi nyengo zotele,” iye waonjezela kunena.

Mutharika wati a Malawi onse mosatengela chipembedzo akuyenela kugwilana manja ndi kuzichepsa pamaso pa Mulungu kuti achitile chifundo dziko la Malawi.

A Mutharika amema atsogoleri a mipingo mu dziko muno kuti atsogolele mtundu wa a Malawi polapa pamaso pa Chauta ndi kumema kuti achitile chifundo dziko la Malawi ndikugwetsa mvula.

Oona za nyengo ati mvula ikuyembekezeleka kumapeto kwa sabata lino. Koma a Malawi ena ataya chikhulipililo mwa akatswiliwa chifukwa ananena chimodzimodzi sabata latha.

 

 

 

Advertisement