Mitengo ya madzi yakwera

Advertisement

Pamene anthu akudandaula kale ndi kukwera kwa mitengo yazinthu zambiri, boma kudzera kuunduna wa zachilengedwe laloleza mabungwe ogulitsa madzi mdziko muno kukweza mitengo.

Izi ndimalingana ndi chikalata chomwe undunawu watulutsa posachedwapa chomwe wasainira ndi mlembi wamkulu kuundunawu a Yanira Mtupanyama.

Mumchikalatachi, a Mtupanyama anati undunawu waloleza makampani ogulitsa madziwa ati kaamba koti mabungwe ogulitsa madziwa akukumana ndimavuto osiyanasiyana kaamba kakukwera kwa zinthu.

Apa iwo anapeleka chitsanzo cha kukwera mtengo kwa mankhwala omwe amathira mu madzi kupha tizilombo komaso kukwera mtengo kwa magetsi zomwe akuti zikupangitsa kuti mabungwewa asamapange phindu lili lonse.

Iwo ati akukhulupilira kuti kukweza mitengoku kuthandizira mabungwe ogulitsa madziwa kuti akwanitse kugwira ntchito yawo bwino ponena kuti mitengo yakale imapeleka chiopsezo kuti zinthu zina zitha kusokonekera.

A Mtupanyama anaonjezeraso kuti undunawu walora mabungwe ogulitsa madziwa kukweza mitengoyi kaamba koti komaliza mabungwewa kukweza mitengoyi zinali zaka zitatu zapitazo.

Mabungwe ogulitsa madziwa akweza ndi K50 pa K100 iliyose ndipo mitengoyi ati ikugwira ntchito kuyambira pa 1 November.

Pakadali pano aMalawi ambiri makamaka pamasamba amchezo ati ndiokhumudwa ndikukwera kwa mitengoku ponena kuti akukumana kale ndizipsinjo zina kaamba kakukwera kwa mitengo yakatundu wina.

Water boards in Malawi increase water tariffs

 

 

Advertisement