Munditukwaniranji? Walira mokweza Lazaro

Advertisement

Mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera, yemwe omunyadira amangoti Lazaro, wadandaula kuti a Malawi akumamutumizira mauthenga omunyoza pa nambala yake ya WhatsApp kamba koti iye akulephera kuyendetsa dziko lino.

Poyankhula pomwe amatsekulira ndondomeko ya chitukuko ku Lilongwe, A Chakwera anati pali anthu ena ambiri omwe amawatumizira mauthenga pa foni yawo kuwatukwana.

Iwo anonjezera kunena kuti ena amapempha thandizo la mabanja awo ndipo amafika pomawaopseza kuti ngati sawathandiza sadzawavotelaso.

“Zinthu sizisintha ngati aliyense azingoyembekezera kuti ena ndi omwe asinthe zinthu. Ndili ndi mauthenga oposa 500, ndiyendetse banja la aliyense kuchokera ku Chitipa mpaka ku Nsanje pakuti ndine pulezidenti.

“Wina ananditukwana kuti ‘moti lero basi osandiyankha WhatsApp yanga’. Ndakhala munomu ndalandira ma message mwina 100. Ndiye nditati ndikhale pa phone tsiku lonse ndibwera kuno? Chibwana chenicheni, dziko sitikweza pa WhatsApp. Tiyeni tonse tigwire ntchito,” anatero a Chakwera.

A Chakwera anaonjezera kuti anthu omwe amawatumizira mauthenga pafoni yawo asayembekeze kuti adziwayankha uthenga uliwonse ponena kuti ngati atakhala bize ndifoni, mapeto ake zitukuko zambiri sizichitika mdziko muno.

Malawians want me to run their families – Chakwera  

 

 

 

Advertisement