Matenda a mphere abuka ku Blantyre

Advertisement
Malawi24.com

Ofesi ya zaumoyo ku khonsolo ya m’boma la Blantyre, yatsimikiza kuti m’madera ena a m’bomali mwabuka matenda a mphere omwe posachedwapa anasautsa ku Dedza ndi Lilongwe.

Izi ndi malingana ndi chikalata chomwe ofesi ya zaumoyoyi yatulutsa Lolemba chomwe chasainidwa ndi mkulu wa zaumoyo m’bomali, Dr. Gift Kawalazira.

Mumchikalatachi, Dr Kawalazira ati kuchokera mwezi wa June kufika mwezi wa September chaka chino, m’bomali mwapezeka anthu 255 omwe akudwala matendewa omwe kwambiri zimakhala zilonda za pakhungu.

Mkuluyu wati ena mwa madera omwe nthendayi yabuka ndimonga: South Lunzu komwe akuti kwapezeka anthu 69, ku Chichiri prison komwe akuti kwapezeka anthu 9 pamene kudela la Kadidi akuti kwapezeka anthu 17 omwe akudwala nthendayi.

Iwo ati madera ena ndimongaso: Makata komwe kwapezeka anthu 20, Zingwangwa anthu 9, Lighthouse anthu 8, Dziwe anthu 5, Mpemba anthu 17, Chimembe anthu awiri, Gateway anthu 61 pamene zipatala zoyendayenda zapeza anthu 38 omwe akudwala nthendayi.

“Ofesi yazaumoyo ku Blantyre ikufuna kudziwitsa anthu kuti yapeza kuti chiwerengero cha anthu omwe akupezeka ndi matenda a mphere, chikukwera mumzipatala zina za m’bomali,” yatelo mbali ina ya chikalata chomwe asainira Dr Kawalazira.

Pakadali pano ofesiyi yati anthu m’bomali asadele nkhawa ponena kuti ili ndi mankhwala ochuluka ndipo yalangizaso anthuwa kuti adziwitse azaumoyo ngati akukaikira kuti wina akudwala nthendayi.

Nthenda ya mphere imadza kaamba kakusowekera kwa ukhondo makamaka wapakhungu ndipo imafalitsidwa pomwe munthu yemwe akudwala nthendayi wagunda mzake yemwe sakudwala.

Matendawa, anayamba kugwa m’maboma achigawo chapakati makamaka m’maboma a Lilongwe ndi Dedza miyezi iwiri yapitayi.

Advertisement