Anthu okwiya atentha tchalichi

Mapemphero anasokonekera dzulo pa mpingo wa Headstone Prophetic Ministry International ku Chileka mu mzinda wa Blantyre pamene anthu omwe akuwaganizira kuti ndi a gulewamkulu atentha tchalitchi.

Malingana ndi ofalitsa nkhani pa polisi ya Chileka a Sergeant Jonathan Phillipo, nkhaniyi yachitika mmawa wa Lamulungu pa 17 October pomwe anthu okwiyawa anakhamukira ku tchalitchichi chomwe amatsogolera ndi ambuye Overtone Makuta.

A Sergeant Phillipo anati anthu okwiyawa omwe ananyamula zikwanje komaso zitsulo, atafika pamalopa analamura kuti anthu onse omwe anali mkati mwa mapemphero, atuluke mutchalitchichi ndipo pamapeto pake anayamba kutentha tchalitchichi.

Tchalitchi cha Headstone Prophetic Ministry International

Iwo ati zida zoyimbira zampingowu zawonongedwa komaso galimoto ya m’modzi mwa mamembala a mpingowu yomwe inali panja, yatenthedwa nawo.

Mneneri wa apolisiyu wati nkhaniyi ikutsatira nkangano omwe unabuka masiku angapo apitawa potsatira imfa ya a Group Village Headman Nkata omwe akuti kupatula kukhala membala wa mpingowu amapitaso ku gule wamkulu.

“Ndizoonadi kuti Lamulungu anthu ena okwiya atentha tchalitchi cha Headstone Prophetic Ministry International ku Chileka kuno pankhani yokhudza imfa ya amfumu athu a Nkata omwe akuti amapemphera kumpingowu komaso anali membala wa gule wa mkulu.

“Mfumuyi itamwalira mbali zonse zinkafuna kuyendetsa mwambo wa malirowo koma a mpingowa ndiomwe anayendetsa zonse zomwe sizinasangalatse otsatira gule wa mkuluyu ndipo zikuoneka kuti izi achita kaamba kamkanganowu,” atelo a Phillipo.

A Phillipo anati pakadali pano kafukufuku adakali mkati kuti adziwe kuti ndikatundu wa ndalama zingati yemwe waonongeka pa chipolowechi koma ati pano apolisiwa amanga anthu atatu powaganizira kuti anatenga nawo gawo pakutenthedwa ka tchalitchichi.

Advertisement