A Nankhumwa ati boma lichotse misonkho pa mafuta a galimoto

Advertisement

Mtsogoleri wotsutsa boma a Kondwani Nankhumwa alangiza boma kuti lichotse ina mwa misonkho yomwe inayikidwa pa mafuta a galimoto ponena kuti ndiyomwe ikupangitsa kuti mafutawa akhale okwera mtengo kwambiri.

A Nankhumwa amayankhula izi atayendera ina mwa misika yamumzinda wa Blantyre komwe ati amafuna akaone m’mene kukwera kwa mafuta agalimoto kwakhudzira anthu ochita malonda.

Ina mwa misika yomwe anayendera ndi monga msika wa Limbe, Ndirande, nsika waukulu mutawuni ya Blantyre komaso anakafika ku Chichiri shoprite ndipo pamapeto pake anapangitsa msonkhano wa atolonkhani.

A Nankhumwa kuona mitengo ya zinthu mu shop

A Nankhumwa kuona mitengo ya zinthu mu shopPoyankhula pa msonkhanowu, a Nankhumwa omweso ndi wachiwiri kwa mtsogoleri wa chipani cha DPP mchigawo chakummwera, anati kukwera kwa mafuta agalimoto kwapangitsa kuti ochita malonda ambiri akumane ndizikhomo.

Iwo anati awuzidwa ndi ochita kabaza, oyendetsa maminibasi, mavenda, ogulitsa malonda omwe anakumana nawo kuti momwe mtengo wa mafuta agalimoto akweramu, zinthu zambiri zakweraso mtengo zomwe zapangitsa moyo kukhala owawa.

Apa iwo anati ndi kwabwino kuti boma liganize njira zomwe zingapangitse kuti mafuta agalimoto atsike mtengo zomwe anati zina mwa izo ndikuchotsa misonkho ina yomwe bomali linaika pa mafutawa.

“Ndinayendera ena mwa madera a mumzinda wa Blantyre kuti ndikaone ndekha zomwe anthu akukumana nazo makamaka kaamba kakukwera mtengo kwa mafuta agalimoto ndipo ndaona ndimaso anga kuti zinthu sizili bwino. Anthu akuvutika kwambiri.

“Ine langa ndipempho kupita kuboma kuti pali misonkho ina yomwe inaikidwa pa mafuta, nde ndimati kwapano boma lichotse misonkho imeneyo chifukwa ndiimene yapangitsa kuti mtengowu ufike pamene ili pano chomwe ndi chipsinjo kwa aMalawi,” atelo a Nankhumwa.

Mkuluyu wauzaso mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera kuti pamodzi ndi nduna zawo achepetse maulendo opita kunja komaso ozungulira m’dziko muno ponena kuti maulendo ngati amenewo, boma limaononga ndalama zambiri zomwe zitha kugwira ntchito iana.

Apa a Nankhumwa anati ndalama za maulendo ngati amenewo boma litha kuziyika kuthumba lamafutawa ndipo pamapeto pake mtengo siungakwere kwambiri ngati momwe wakwelera pano.

“Ndikufuna ndiwapemphe a Chakwera ndi nduna zawo kuti achepetse maulendo opita kunja komaso ozungulira m’dziko muno ndipo ndalama zake zithandize kuchepetsa mtengo wa mafutawa makamaka mu nyengo ino ya mlili wa covid-19,” anawonjezera choncho a Nankhumwa.

Pakadali pano mafuta a petulo akugulitsidwa pa K1,150 kuchoka pa K899.20 pamene dizilo ali pa K1,120 kuchoka pa K898 ndipo palafini alipa K833.20 kuchoka pa K719.60 zomwe zapangitsa kuti mitengo yamayendedwe komaso katundu wina akwere mtengo.

Advertisement

2 Comments

  1. Komaso mkuyang`ana ku mafuta agalimoto okha bwanji ophikilawa chifukwa osaukawa akati anyera ndiwo zokoma zimakhala athilamo mafuta ophikila koma pano akuvuta komaso akudula kuposa agalimotoyo, komaso ndizoona kuti msonkho wamafutawo ukachosedwa kwati maphunziro aja aziyendabe bwino koma? yes kuchosa msonkho wa mafuta skofunika than kubwezeretsa misonkho ya ogwira ntchito

  2. Apatu nkuluyu wankhula za nzeru. Chifukwa ndiye tapsyinjikadi. Koma a Nankhumwa tatiyankhani. Kodi akachotsa misonkho kumafuta, Boma litani kuti lipeze ndalama zomwe linakapeza kuchokera kuchokera Ku mafuta. Izi ndafusa chifukwa tikudziwa bwino lomwe kuti Boma limadalira misonkho ngati iyi kuti litumikile a Malawi monga kuchipatala, kumamphuziro, kumanga misewu, zaulimi, chitetezo ndi zitukuko. Komanso munakanenako kuti inuyo simudura ndi ma MP azanu simudura misonkho ngakhale mumalandira salary ndi ndalama zina zoti Boma litha kulipira aphunzitsi opitilira 100 pa mp m’modzi, bwanji mutakapempha kuti nanu azikudurani misonkho kuti ipangitse m’malo kwake Boma lichotse misonkho Ku mafuta. A lidala otsutsa tiuzeninso amalawi kuti ngakhale kuyenda kwanu ukuku mwagwiritsa ntchito ndalama za Boma chifu galimoto ndi mafuta omwe mwagwiritsa ntchito nga Boma, muli ndi security ya Boma, muli ndiokuthandizilani waboma.

Comments are closed.