Mr Jokes apepesa poselewura a Mutharika

Advertisement

M’modzi mwa akatswiri ochita zisudzo mdziko muno Andrea Thonyiwa amene amadziwika ndi dzina loti Mr Jokes, wapepesa kwaotsatira chipani chotsutsa cha DPP kaamba ka kanema yemwe anatulutsa oselewura momwe amayankhulira a Peter Mutharika.

Mukanema yemwe anthu akugawana pamasamba amchezo ndipo tsamba lino tamuwona, akuonetsa katswiri ochita nthabwalayu akuyelekeza m’mene a Mutharika amayankhulira.

Mkanemayu Mr Jokes akuti mtsogoleri wakaleyu amatha kuyankhula pamsonkhano wa ndale, kuyamba mpaka kumaliza koma anthu osamva ngakhale chimodzi pazomwe amayankhulazo.

“Pulezidenti yemwe analamulira dziko la Malawi amene sindidzamuiwala ndi Peter Mutharika. Peter Mutharika amapangitsa nsonkhano, anthu ndikubwera, kudzadza, iye kuyankhula, anthu osamva.

“Imvani sipitchi ya Peter: leyi mjemeni, zikokambi………..­…… Zikokambi. Iwe ndikumufusa mzako kuti kapena iwe wamva, iye mkudzati amwene tiyeni tikangogule madzi. Peter Mutharika, takusowani kwambiri,” inatelo mbali ina ya kanemayu.

Koma patangodutsa maola ochepa atatulutsa kanemayu, Thonyiwa wabwera poyera polemba patsamba lake la Facebook ndikupepesa otsatira chipani cha DPP ponena kuti samadziwa kuti kanemayu angawakhumudwitse.

Mr Jokes omwe akuoneka kuti anaopsezedwa ndi anthu ena kaamba kopanga kanemayu, anati iwo anapanga kanemayu pongofuna kusangalatsa anthu ndipo walonjeza kuti sadzapangaso.

“Uthenga uwu ukupita kwa akuluakulu a DPP komaso ma membala onse. A zimayi ndi azibambo, ndikufuna ndipepese kaamba ka kanema amene ndinapanga yemwe ndinatchulamo mtsogoleri wanu a Peter Mutharika.

“Sindimadziwa kuti izizi zikupwetekani. Mapulani anga anali oti ndingosangalatsa anthu koma kaamba koti mwaona kuti ndinalakwitsa, ndikuti pepani. Sindidzachitanso, chonde ndikhululukileni,” apepesa choncho Mr Jokes.

Advertisement

One Comment

  1. Uli boo jocks kumene sizimaveka zoyakhula zake(monga tidzatsegula kampani yophwinya mapeyala, ndiye kuti chani tanenani inuyo a dpp?? 🤣🤣🤣🤣🤣🤣🤣

Comments are closed.