A Mpinganjira ati chilango chachuluka, akukasuma

...ACB yati ikapempha khothi lionjezera chilangochi...

Mponda matiki Thomson Mpinganjira yemwe wagamulidwa kukaseweza jele kwazaka zisanu ndi zinayi (9) wati sakukhututsidwa ndichigamulochi ndipo akuti akamang’ala kubwalo Supreme.

A Mpinganjira omwe anapezeka olakwa pa mlandu ofuna kunyengelera oweruza milandu kuti akhotetse chigamulo pa mlandu chaka chatha, alandira chiweruzochi lachiwiri pa 5 October, 2021 mumzinda wa Blantyre.

Popeleka chilangochi, oweruza milandu Dorothy DeGabrielle anati zomwe ankafuna kuchita a Mpinganjira zinali zolakwika kwambiri ndipo anati khumutchayu amayenera kulandira chilango chamtunduwu kuti enaso omwe ali ndikhalidwe longa lawoli atengelepo phunziro.

Koma poyankha pachilango chomwe chapelekedwa kwa a Mpinganjira, yemwe amawaimilira pa mlanduwu, a Patrice Nkhono ati a Mpinganjira kudzera kwaiwo akagwadwa ku bwalo la Supreme.

A Nkhono anena kuti chigamulo komaso chilango chomwe bwaloli lapeleka kwa mponda matikiyu sichikuwagwira mtima.

Iwo anawuza atolankhani omwe anakhamukira kubwalori kuti akuona kuti panalibe umboni omwe unapelekedwa pakupezeka olokwa kwa a Mpinganjira ndipo atiso chilango chomwe chapelekedwa ndichachikulu kwambiri.

“Zifukwa zambiri tinanena kale mmene mulanduwu umavedwa muja. Kuwapeza olakwa Dr Mpinganjira umboni wake panalibepo komaso tinawapatsa a judge mfundo zoti awaganizile koma sanalembe mkulemba komwe.

“Komaso pamwamba pazonsezi tikunena kuti bwalori lapeleka chilango chachikulu kwambiri chosagwirizana ndi mlanduwu. Choncho tikuona kuti zonsezi zikaganizilidweso ku bwalo la Supreme,” atelo a Nkhono omwe amaimilira a Mpinganjira pa mlanduwu.

A Mpinganjira ayamba kuseweza jele ku ndende ya Chichiri mumzinda wa Blantyre ndipo pamene mkuluyu amakalowa mgalimoto ya polisi yomwe inakawasiya ku ndendeku, achibale awo ena analephera kudzigwira ndipo ena anayamba kulira.

Pakadali pano, yemwe amaimilira boma pamlanduwu, solicitor general Reyneck Matemba wati bungwe la ACB lomwe linatengera nkhaniyi ku kubwaloli lati ndilokhutitsidwa ndichilangochi koma iwo ati bungweli lilitchelu pa maganizo a mponda matikiyu.

A Matemba ati izi zikusonyeza kuti mkuluyu sakuonetsa kugonja ndipo ati ngatidi nkhaniyi ingatengeredwe ku bwalo la Supreme, iwo akapempha oweruza mlanduwu kumeneko kuti awonjezere chilangochi.

Advertisement