Boma lati linafusa kaye lisanakweze mtengo wa feteleza


Boma la Malawi lati linayamba lafusa kaye kumbali zonse zokhudzidwa ngati kunali koyenera kukweza mtengo wa feteleza mundondomeko yazipangizo zaulimi zotsika mtengo, AIP, ndipo lati alimi ena amati panalibe vuto mtengo olo ukanafika pa K10,000.

Izi ndimalinga ndi nduna ya zofalitsa nkhani a Gospel Kazako omweso ndi mneneri wa boma ndipo amayankhula Lachinayi pamsonkhano wa atolankhani komwe unduna wa zaulimi unalengeza zakusintha kwa mtengo ogulira feteleza.

Pansonkhano wa atolonkhaniwu boma lati thumba la feteleza lomwe chaka chatha limagulidwa pamtengo wa K5000, pano lizigulidwa pa K7500 ndipo layika K27,000 ngati mtengo wa feteleza osatsika mtengo.

Poyankhula pamsonkhano wa atolonkhaniwu, a Kazako anati mtengo watsopanowu usanakhazikitsidwe, maunduna okhudzidwa anafusa kaye maganizo ambali zonse ponena kuti boma la a Chakwera ndiboma lokhalo lomwe limapeleka ufulu kwa mzika zake.

Iwo ati alimi ena amauza unduna wa zaulimi kuti panalibe vuto mtengo wa fetelezawu unakafika pa K10, 000 koma boma linaona kuti lisakweze choncho poganizira kuti mtengowo unakakhala okwera kwa alimi ena.

“Enatu omwe tawafunsa amachita kunena kuti olo munakaika mtengo-wo pa K10,000 ena amati ai uikeni pa K8000 ife tikwanitsa, koma ayi boma la a Chakwera laika mtengo umenewu wa K7500,” atelo a Kazako.

Nduna ya zofalitsa nkhaniyi inadzudzulaso mchitidwe ongotsutsa chili chonse chomwe boma lanena ponena kuti mchitidwewu uli ndikuthekera kobwezeretsa zinthu zina mmbuyo.

A Kazako anatiso anthu ayembekeze kuti pakhala kumangidwa kwa onse omwe satsatira zomwe boma lanena pamtengo wafeteleza otsika mtengo ngakhaleso osatsika mtengo.

One comment on “Boma lati linafusa kaye lisanakweze mtengo wa feteleza

Comments are closed.

Discover more from Malawi 24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading