Matenda a mphere avuta ku Dedza

Akuluakulu a ofesi ya zaumoyo ku khonsolo ya m’boma la Dedza atsimikiza kuti madera a m’bomali mwabuka matenda a zilonda zapakhungu omwe ndi kuphatikizapo mphere zomwe ati zagwira anthu ochulukirapo.

Malingana ndi ofalitsa nkhani ku ofesi ya zaumoyo m’bomali a Mwayi Liabunya, nkhaniyi ikutsatira zotsara za kuyezedwa kwa anthu ena omwe akudwala matenda apakhunguwa.

A Liabunya anauza imodzi mwa nyumba zofalitsa nkhani mdziko muno kuti mwa odwala 2475 omwe anayezedwa miyezi iwiri yapitayo, anthu 2099 ndiomwe atsimikizika kuti akudwaladi matenda a mphere.

Iwo anaonjezera kuti apezaso kuti mwa anthu omwe anayezedwawa, 376 sakudwala mpherezi koma ati anthuwa akudwala matenda ena azilonda za pakhungu ndipo zadziwika kuti matendawa akhudza kwambiri msukulu za primary komaso m’midzi.

Ofalitsa nkhaniyu wati pakadali pano ofesi yawo ikuyendera mzipatala komaso mmidzi ina ya m’bomali kupeleka thandizo la mankhwala kwa anthu onse omwe akhudzidwa ndi matendewa.

“Ntchito imeneyi tinapeza anthu okwanira 2475 omwe anali ndi matenda osiyanasiyana apakhungu ndipo pa anthu amenewawa, anthu okwana 2099 ndiomwe zatsimikizika kuti matenda ake ndi a mphere pamene anthu 376 akudwala matenda ena apakhungu.

“Pakadali pano tafika ku zipatala zokwanira zisanu zomwe ndi; Kalulu, Thyolo, Mayani, Mthini ndi Chiphwanya,” atelo a Liabunya.

Ofesi yazaumoyo m’bomali yapempha anthu onse kuti aonetsetse kuti akutsatira ndondomeko za ukhondo wabwino ndi cholinga chofuna kuthana ndi kufala kwa matendawa

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.