Apolisi asamutsidwa atadandaula zakuchepa kwa ndalama za alawansi ya SADC

Advertisement

Apolisi okwana 40 omwe ena mwaiwo ndi omwe anadandaula zakuchepa kwa ndalama za alawasi pomwe anagwira nawo ntchito yosungitsa bata ku bwalo la ndege la Kamuzu panthawi ya msonkhano wa SADC, asamutsidwa m’malo awo ogwilira ntchito.

Izi ndimalingana ndi chikalata chomwe wa sayinira ndi mkulu owona zolemba ndikuchotsa anthu ntchito kunthambi ya polisi a komishonala Stan Kaliza.

Mumchikalatachi chomwe chatulutsidwa Lachiwiri pa 31 August, akuluakulu apolisiwa sanapeleke tsatane tsatane wa zifukwa zomwe apolisiwa asamutsidwira komaso tsamba lino lamvetsedwa kuti apolisiwa sanapatsidwe nthawi yokozekera nsamukowu.

Poyankhulapo zankhaniyi, mneneri wa nthambi ya polisi a James Kadadzera ati ndikovuta kuti nthambiyi inene tsatanetsatane wakusamutsidwa kwa anthuwa ponena kuti nkhani za nthambi ya polisi ndizokhudza chitetezo choncho nkhani zina sangakambe pagulu.

“Nkhani zankati mwa polisi sitimazikambirana kunja, kutelo ndikuphwanya malamulo athu omwe timatsatira ku polisi kuno,”atelo a Kadadzera.

Nkhaniyi ikutsatira pomwe ena mwa apolisi omwe asamutsidwawa anaitanidwa kulikulu la nthambi ya apolisi ku Lilongwe ati kaamba kodandaula zakuchepa kwa ndalama ya ma alawasi yomwe anapatsidwa.

Apolisiwa anadandaula ndi ndalama yokwana K30,000 yomwe anapatsidwa pa ntchito yomwe anagwila yosungitsa bata kwa masiku khumi panthawi ya nsonkhano wa SADC omwe umachitikira mumzinda wa Lilongwe.

Apolisiwa anauza imodzi mwanyumba zoulutsira mawu mdziko muno kuti apolisi ena omwe ndi amaudindo ofanana ndi iwo analandira ndalama za pakati pa K130,000 ndi K300,000 pomwe iwo apatsidwa ma K30,000 basi.

Advertisement