Apolisi 45 ayitanidwa atadandaula zakuchepa kwa maalawansi

Advertisement

Apolisi okwana 45 omwe anagwira nawo ntchito yosungitsa bata ku bwalo la ndege la Kamuzu panthawi ya msonkhano wa SADC ayitanitsidwa kulikulu la nthambi ya apolisi ku Lilongwe ati kaamba kodandaula zakuchepa kwa ndalama ya maalawasi yomwe apatsidwa.

Lachitatu apolisiwa anadandaula ndi ndalama yokwana K30,000 yomwe anapatsidwa pa ntchito yomwe anagwila yosungitsa bata kwa masiku khumi panthawi ya nsonkhano wa SADC omwe umachitikira mumzinda wa Lilongwe ndipo watha Lachitatu.

Apolisiwa anauza imodzi mwanyumba zoulutsira mawu m’dziko muno kuti apolisi ena omwe ndi amaudindo ofanana ndi iwo akulandira ndalama za pakati pa K130,000 ndi K300,000 pomwe iwo apatsidwa ma K30,000.

Ndipo potsatira izi, Lachinayi m’mawa, apolisiwa ayitanitsidwa kulikulu la a polisi ku Area 30 ku Lilongwe komwe akuyembekezeka kukumana ndi akuluakulu osungitsa mwambo ku nthambi ya apolisi.

Ngakhale watsimikiza zankhaniyi, mneneri wa apolisi mdziko muno a James Kadadzera ati ndizokhumudwitsa kuti apolisiwa anasankha kukadandaula za mavuto awo kwa atolonkhani m’malo motsata njira zoyenera.

“Ku polisi kuno tili ndondomeko zimene timatsatira pakakhala kuti pali madandaulo aliwose ndipo wa polisi aliyese amadziwa zazimenezo. Nde ngati pali apolisi ena omwe abwera kwa inu kudzadandaula zamavuto awo, auzeni kuti atsate ndondomeko yomwe inakhazikitsidwayo,” watelo Kadadzera.

Pakadali pano sizikudziwika kuli apolisiwa apatsidwa chilango chotani ngati angapezeke olakwa pankhaniyi.

M’mbuyomu apolisi ochuluka akhala akusamutsidwa m’malo awo antchito ndikupititsidwa kumamidzi kaamba kodandaula za mavuto ena omwe amakumana nawo.

Advertisement