Apolisi adzudzulidwa pomanga a Namiwa mwankhanza

Advertisement

M’modzi mwa anthu omwe amayankhulapo pankhani zokhudza chitetezo cha mdziko a Sherrif Kaisi adzudzula apolisi kaamba komanga omenyera ufulu a Sylvester Namiwa mwankhanza.

A Namiwa amangidwa Lachitatu pomwe amatsogolera zionetsero zomwe cholinga chaka chinali kufuna kuti akuluakulu a nyumba yamalamulo komaso mtsogoleri wa dziko lino achitepo kanthu pa kuzembetsedwa kwa bilu yokhudza ngongole.

Malingana ndi kanema yemwe tsamba lino laona a Namiwa anamangidwa atamaliza kuyankhula ndi atolankhani kunja kwa nyumba yamalamulo yomwe ili pamalipande ochepa ndiku BICC komwe kukuchitikira msonkhano wa SADC.

Kanemayu akuonetsa a Namiwa atagwidwa mwamphamvu ndi mzibambo ovala suti kenako mothandizidwa ndi apolisi omwe anavala yunifolomu iwo anaduduluzidwira ku galimoto yomwe inachoka pamalopa mwaliwiro itanyamula omenyera ufuluyu kukamutsekera.

Ndipo poyankhulapo pakumangidwa kwa mkuluyu, a Kaisi omwe amayankhula pankhani zachitetezo, ati apa apolisi samaenera kumanga mkuluyu mwantundu otelewu ponena kuti a Namiwa sanaonetse mavuvu ali onse.

A Kaisi awuza tsamba lino kuti zomwe achita apolisi ndikuphwanya malamulo omwe amayenera kutsatidwa pomwe apolisi akufuna kumanga munthu yemwe walakwira malamulo a dziko lino.

“Zomwe tikuona apa zikusonyeza kuti apolisi sanaonetse ukadaulo wawo kaamba koti akamamanga munthu pamayenera pachitike kaye zinthu zingapo zomwe pakumangidwa kwa a Namiwa sizinachitike.

“Poyambilira munthu amene sakuchita mavuvu amayenera awuzidwe kuti ‘takumanga’. Akakhala kuti akuchita makani kapena akuthawa ndipomwe apolisi amagwiritsa ntchito mphamvu ndikumufinya munthuyo kuti amumange koma samayenera kungofikira kumufinya munthu ngati momwe zakhaliramu, ayi,” atelo a Kaisi.

Iwo atiwuza kuti zomwe achita apolisi pomanga a Namiwa mwamavuvu zili ndikuthekera koti zitha kuonongaso ubale wabwino omwe unalipo pakati apolisi ndi anthu mdziko muno ndipo apempha akuluakulu apolisi kuti awonetsetse kuti mchitidwewu utheletu.

“M’mbuyomu munachitika ma zosintha zomwe cholinga chake kunali kupanga polisi kuti ikhale paubale ndi anthu, ndipo mchifukwa chaka pano imatchedwa Malawi Police Service. Tsono polisi siikuyenera kutembenukaso lero ndikumazuza anthu, ayi,” anaonjezera choncho a Kaisi.

A Kaisi atiso izi zimapangitsa kuti anthu azidana ndi mtsogoleri wadziko.

“Ine ndimafuna ndiwapemphe apolisiwa kuti asatukwanitse mtsogoleri wadziko a Lazarus Chakwera chifukwa siimane wawatuma kupanga khalidwe limeneli ngakhaleso kumenya anthu pofuna kuti avale mask, izi zithe,” anatero a Kaisi.

Mneneri wa Polisi a James Kadadzera ati apolisi amanga a Namiwa cifukwa choti amachita zionetsero popanda chilolezo kuchokera ku khonsolo ya mzinda wa Lilongwe.

Apolisi anamanganso a Edwin Mauluka, omwe ndi mkulu wa zofalitsa nkhani ku bungwe la CDEDI lomwe limatsogoleledwa ndi a Namiwa, atapita kukawazonda a Namiwa ku polisi komwe akusungidwa ku area 30 ku Lilongwe.

Advertisement