Mwana wa a Chakwera akupita nawo ku UK

Advertisement

Mwana wa mtsogoleri wa dziko lino Violet Chakwera  ali pa mndandanda wa anthu khumi omwe akupelekeza a Lazarus Chakwera ku United Kingdom.

A Chakwera akuyembekezeka kunyamuka mdziko muno Lamulungu pa 25 July kupita ku UK ku mkumano wa maphunziro omwe uyambe pa 28 ndikutha pa 29 July omwe akutsogolera ndi nduna yaikulu ya dzikolo a Boris Johnson komaso mtsogoleri wa dziko la Kenya a Uhuru Kenyatta.

Koma chadabwitsa anthu kwambiri mchakuti mtsogoleri wa dziko linoyu waika mwana wake Violet pa mndanda wa anthu khumi omwe akumupelekeza kumkumanowu pamene nduna yowona zaubale wa dziko lino ndi maiko akunja a Eisenhower Mkaka sakupita nawo.

Nkhaniyi itadziwika kumene, manong’onong’o pamasamba amchezo anaveka kuti Violet akupita nawo paulendowu kulowa mmalo mwa a Mkaka koma boma latsutsa mwantu wagalu.

Malingana ndi a Mkaka, Violet akupita nawo kuulendo kaamba koti pali ntchito Ina yoti akagwire ndipo kusapita nawo kwaiwo ndi kaamba koti akuyenera kupita mdziko la Morocco komwe ati kuliso msonkhano wina ofunika.

“Zoona zake nzakuti sakupita mmalo mwa ine. Akupitadi apaulendowu koma osati mmalo mwa ine. Lamulungu lomwe akunyamuka apulezidenti naneso ndili ndi ulendo wanga waku Morocco choncho nchifukwa chaka sindinawapelekeze nde tinangoganiza zogawana maulendowa,” atelo a Mkaka.

Nkhaniyi yaonjezera mkwiyo omwe anthu ali nawo kaamba koti posachedwapa anthu anadzudzula mtsogoleriyu kaamba kosankha mwana wakeyu kukagwira ntchito ku ofesi ya oyimilira dziko lino ku Brussels.

Pakadali pano, anthu m’masamba amchezo akupitilira kudzudzula a Chakwera ati kaamba kosathetsa khalidwe lakondera lomwe ankadzudzura pomwe anali mtsogoleri wazipani zotsutsa boma.

Advertisement