Katemela wa Covid-19 walephera kufika lero

Advertisement

Dziko la Malawi lalephera kulandira katemera wa Covid-19 wa AstraZeneca yemwe amayenera kufika mdziko muno lero.

Watsimikiza za nkhaniyi ndi nduna ya zaumuyo a Khumbize Kandodo Chiponda omweso ndi wa pampando wa komoti yamrsogoleri wadziko yotsogolera ntchito yolimbana ndi matenda a covid-19.

Malingana ndi a Kandodo Chiponda, katemerayu yemwe akugulidwa mdziko la India, walephera kufika lero mdziko muno kaamba ka zovuta zina ndipo ati pakadali pano sizikudziwika kuti katemerayu afika liti mdziko muno.

“Ndizoonadi kuti timayenera kulandira katemera wa covid-19 lero monga momwe ndinanenera sabata yatha koma zalepheleka kaamba kazovuta zina padongosolo loti katemerayu afike kwathu kuno.

“Likamatha tsiku lalero ndi pomwe tingathe kudziwa kuti katemerayu afika liti kuno komano ndiwatsimikizile aMalawi kuti katemerayu ananyamuka kale komwe tikumugula choncho anthu asadere nkhawa, katemerayu afika posachedwapa,” atelo a Kandodo Chiponda.

Kubwera kwa katemerayu yemwe ndi 192,000, kukutsatira kutha kwa katemerayu mdziko muno kaamba ka kuchuluka kwa anthu omwe anakabaitsa mundime yachiwiri yobaitsa katemerayu.

Malingana ndi azaumoyo, katemelayu akumathandiza kuti munthu asakhale pa chiopsezo chodwalika kwambiri pomwe watenga kachirombo ka korona.

Katemerayu wagulidwa ndi thandizo lochokera ku United Nations (UN) komaso United Nations Children’s Emergency Fund (UNICEF)

Advertisement