Boma libweza njinga zamoto zomwe linalanda

Advertisement

Boma kudzera kuunduna wazachitetezo cha mdziko lalengeza kuti kuyambira Lachiwiri sabata yamawa likhala likubweza njinga zamoto zonse zomwe linalanda.

Izi ndimalinga ndi nduna ya za chitetezo chamdziko a Richard Chimwendo Banda omwe amayankhula kunyumba yamalamulo Lachinayi pa 8 june, 2021.

A Chimwendo Banda anati boma lapanga chiganizochi polingalira kufunika kwanjingazi pankhani za mayendedwe mdziko muno ndipo ati njingazi zibwezedwa kwa eni ake popanda kupeleka chindapusa chilichose.

Ndunayi yati unduna wazamayendedwe wapanga dongosolo loti anthu onse oyendetsa njinga zamoto aziphunzitsidwa kayendedwe koyenera kapansewu ndi cholinga chofuna kuchepetsa chiwerengero cha ngozi za njingazi zomwe zinachuluka pakatipa.

Iwo ati mundondomekoyi, boma lakambilana ndi bungwe lina lamdziko muno kuti idziphunzitsa anthu wa amene angayendere ndi njinga zamoto panseweu koma pamtengo otsika wa K20,000 osati K150,000 ngati mmene zimayenera kukhalira.

Apa ndunayi yatiso anthuwa akabwezeledwa njinga zawozi, apatsidwa mwezi umodzi okha kuti akhale atalembetsa njinga zawo komaso apeze zipewa zovala poyendetsa njinga ndipo ati ngati izi sizichitika pakutha panthawiyi, adzalandaso njingazi.

A Chimwendo Banda anauzaso nyumba yamalamuloyi kuti boma likumana ndi akuluakulu abungwe lawoyendetsa njinga zakabaza ndi cholinga choti pasakhale kubelana njingazi pa nthawi yobwezayi.

 

Advertisement