Chakwera, ndiwe tate wa mbava – watelo Mutharika

Advertisement

Ati mukamayenda mumseu ndi kumuona mtsogoleri wa dziko lino muzikhala kuti mukuona tate wa akuba onse ndithu. Watelo mtsogoleri opuma a Peter Mutharika.

Polankhula pa msonkhano wa atolankhani ku nyumba yawo ku Mangochi, a Mutharika ati a Chakwera asokoneza dziko la Malawi ndipo akupanga zinthu zimene ankanyoza nawo a Mutharika.

Lazarus Chakwera
Mutharika: Ndiwe mfumu ya mbamva

“A Chakwera kunasowa 6.2 biliyoni ndipo nkhani yake sanailondoloze bwinobwino. Kenako kunabwela ya 17 biliyoni ndipo mpaka pano mutu wake sukuoneka,” anatelo a Mutharika.

Iwo anapitiliza ndi kubwenzela chipongwe a Chakwera.

“A Chakwera ananditchula ine kuti ndi mtsogoleri wa akuba, koma lero ndikunena nane kuti a Chakwera ndi tate wa mbava mu Malawi muno,” anatelo a Mutharika.

Mwa zina zomwe adandaula a Mutharika ndi kukwela mtengo kwa zinthu, kuchepa mphamvu kwa ndalama ya Kwacha ndi malamulo a nkhanza amene boma la a Chakwera likubweletsa.

Advertisement