Ochita malonda otsuka galimoto apatsidwa masiku 7 kuti asamuke

…Eni galimoto zotsukidwa ku malo osaloledwa azalipira chindapusa cha K5000

Advertisement
Malawi24.com

Khonsolo ya mzinda wa Lilongwe yauza anthu omwe akupangira malonda otsuka galimoto m’malo osaloledwa kuti achoke mu malowa.

Khonsoloyi yapereka masiku asanu ndi awiri kuti anthuwa asiye malondawo. Khonsoloyi yanena izi mchinkalata chawo chomwe anatulutsa lachisanu ndipo chinasainidwa ndi Eliam Banda m’malo mwa mkulu wa nkhosoloyi.

Malingana ndi chikalatachi, anthuwa akuyenera kuchotsa  katundu wawo ndi zomangidwa zilizonse pamalowa pasanathe masiku asanu ndi awiriwa.

Banda anawonjezera ponena kuti ngati anthuwa anyozera chidziwitsochi, nkhosoloyi idzachotsa katundu ndi kugumula zomanga za zawo.

“Nkhosoloyi sidzakhala ndi mlandu pa katundu yemwe angadzawonongeke panthawi yomwe idzagwetse zomangaza za anthu omwe anganyozere chidziwisochi,” Banda anafotoza.

Iwo achenjezanso eni galimoto kuti asiye kutsukitsa galimoto zawo m’malowa poti galimoto iliyonse yomwe idzapedzeka ikutsukidwa pamalopa idzalandidwa ndipo idzabwezedwa kwa eni ake pokhapokha patapelekedwa chindapusa cha K5,000.

Advertisement