Chakwera apemphelela oba ndalama za Covid, angapo anjatwa

Advertisement

Anthu oposa khumi ndi mphambu zinayi (14) anjatwa kamba koganizilidwa kuti anaba ndalama za Covid, ndipo ena ayikidwa m’manja mwa Chauta ndi mtsogoleri wa dziko lino.

Polankhula usiku wa lamulungu kutsatila kutuluka kwa lipoti loona momwe ndalama za Covid zinayendela, Chakwera analengeza kuti boma lake layamba kutsata onse okhudzidwa ndi nkhaniyi.

Iye ananena kuti a polisi atola kale anthu angapo okhudzidwa ndi nkhaniyi. Ananena kuti mmodzi mwa otoledwawo ndi mkulu ogwila ntchito mu ofesi yake.

Malinga ndi malipoti a polisi, anthu okwana 14 ndiwo atoledwa mokhudzana ndi nkhaniyi.

Odziwika kwambiri pa amene atoledwawa ndi a Mzati Nkolokosa amene anali mkulu oona zofalitsa nkhani mu unduna wa zofalitsa nkhani mu ulamulilo wa DPP.

A Nkolokosa amene akhala akunyodola ulamulilo wa Chakwera anatchulidwa mu ma lipotiwa kuti anatenga ndalama zimene ma lisiti sanapelekedwe.

Polengeza zoti a polisi akhala akusesa bwino lomwe anthu onse okhudzidwa, a Chakwera anapemphanso kuti Chisumphi akanthe onse oba ndalama za boma.

 

 

 

Advertisement