Okudya zake alibe mlandu: mkulu oimila boma pa mlandu akufuna Sumbuleta anjatwe

Advertisement

Mkulu oimila boma pa mlandu wauza a polisi kuti achite likiliki ndi mlandu wa amene anali bwana ku nyumba youlutsila mawu ya MBC, a Aubrey Sumbuleta.

A Sumbuleta akuganizilidwa kuti anali kukakamiza Amayi ena ogwila ntchito pa MBC kuti agone nawo kuti akwele pa ntchito olo pena kungowathandiza kumene.

Malinga ndi kafukufuku amene bungwe loona za ufulu wa anthu la MHRC anachita, amayi okwana eyiti anadandaula za khalidwe la a Sumbuleta. Koma Amayi anayi ndiwo anamasuka kuuza bungwelo tsatanetsatane wa khalidwe la a Sumbuleta.

Mmodzi mwa amayiwo anafotokoza kuti atalowa mu ofesi ya a Sumbuleta, iwo adatulutsa chida chawo ndi kumuuza kuti awathandize. Apa ndikuti atamufunsa kuti “akudya izi ndani?” ati poti anali bwenzi wawo wakale mu 1997.

Mu zokhumba zawo a bungwe la MHRC anati mkulu oimila boma pa mlandu aonetsetse kuti a Sumbuleta apeze tsiku lawo mu khoti.

Lero mkulu oimila boma pa mlandu, a Steven Kayuni, wauza a polisi kuti ayambepo ntchito yofufuza a Sumbuleta pa milandu yomwe akuganizilidwa.

Advertisement