Mukapitiliza kuononga zipangizo za Escom, tikukwezelani magetsi — Kambala

Advertisement
Newton Kambala

Inu mukuba mafuta mu ma thiransifoma, ena inu ogwetsa mapolo a magetsi, kaya omapala magetsi mwa chinyengo, mupweteketsa Tonse.

Nduna yoona za mphamvu, a Newton Kambala achenjeza kuti boma la Tonse likweza magetsi ngati a Malawi apitilize kuononga zipangizo za bungwe loona za magetsi la Escom.

Polankhula mu nyumba ya malamulo, a Kambala ati a Malawi akuchita nkhanza bungwe la Escom maka polionongela zipangizo.

“Tsiku lililonse tikumamva kuti kwina kwake thiransifoma yaphulika, izi si zoona,” anadandaula a Kambala.

Iwo anati ma bungwe a za magetsi tsopano alibe ma thiransifoma ongokhala oti ndi kukasinthila malo amenewa.

“Zikapitilila tikakamazika kuti tikweze mtengo wa magetsi,” anaopseza telo.

Mawu awo abwela pomwe a Malawi akhala akudandaula za mtengo wa magetsi. Pakatipa zakhalanso zikumveka kuti a bungwe la Escom anakweza magetsi mwa kachibisila, koma bungweli linatsutsa zimenezo.

Advertisement