Boma lichotsa msonkho pa njinga zamoto

Advertisement

Boma la Malawi lalengeza kuti posachedwapa lichotsa msonkho omwe anthu amapeleka akagula ndikulowetsa mdziko muno njinga za moto kuchokera m’maiko akunja.

Izi ndi malingana ndi nduna ya zachuma a Felix Mlusu omwe amayankhula kunyumba ya malamulo lolemba pa 15 March, 2021 pomwe aphungu akupitilira kukambilana zinthu zina zofunika kuphatikiza mu ndondomeko ya zachuma ya 2020/2021.

A Mlusu anauza nyumba ya malamuloyi kuti boma la Tonse motsogozedwa ndi mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera, amayamikira kwambiri ntchito yomwe njinga zamoto zikugwira mdziko muno.

Iwo ati buzinezi ya kabaza wa njinga zamoto yapangitsa kuti vuto la mayendedwe lichepe ati kaamba koti njingazi tsopano zili ponseponse komaso zikumatha kufika malo ena omwe magalimoto sangakwanitse kufikako.

Apa ndunayi yati boma yachiona kuti ndichinthu chabwino kuti mu mndondomeko ya zachuma yomwe ikubwerayi, lichotse ndalama yomwe anthu amapeleka akamalowetsa njinga zamoto zomwe zagulidwa maiko akunja.

“Ndizoonadi, nkhani imeneyi inakambidwa mnyumba ya malamulo kaamba koti boma la Tonse limalemekeza ntchito yaikulu yomwe njinga makamaka za kabanza zikugwira pankhani ya mayendedwe mdziko muno.

“Nde tikutelo kuti mundondomeko ya zachuma ikubwerayi, tichotsa ndalama ya msonkho yomwe anthu amayenera kupeleka akamalowetsa njinga zamoto zomwe agula kunja, izi tapanga ndi cholinga chofuna kulimbikitsa bizinezi ya kabaza wa njinga za moto,” atelo a Mlusu.

Apa a Mlusu anati sikuti boma liluza kalikonse pachiganizochi koma ati izi zithandizira kuti chuma cha boma chikwere kaamba koti anthu ogula mafuta agalimoto achuluka komaso ati boma lizipeza ndalama zochuluka pakulembetsedwa kwa njinga zamotozi.

Pothilirapo ndemanga zankhaniyi, nduna ya zachitetezo cha mdziko a Richard Chimwendo Banda ati boma lapanga chilinganizo choti chaka chino chisanathe liphunzitse ochita kabaza pamomwe angamayendere panseu.

A Chimwendo Banda ati chiganizochi chabwera poona kuchuluka kwa ngozi zomwe zikumachitika kaamba kosatsatira ndondomeko yakayendedwe ka pansewu zomwe anati ndi kaamba koti ochita kabazawa amasowa upangiri.

Apa ndunayi inatiso izi zithandiza kuchepetsa chiwerengero cha ochita kabaza wa njinga zamoto omwe akumachitilidwa chiwembu panthawi ya ntchito yawo

Advertisement