Eni minibasi akweza mtengo

Advertisement
Minibus Malawi

Anthu oyenda maulendo osiyanasiyana pa Minibasi kuyambira lero ayamba kulipira mtengo okwelerapo kamba ka kukwera kwa mtengo wamafuta a galimoto m’dziko muno kuchokera lolemba.

Kalata yomwe alemba eni Minibasiwa pasi pa bungwe lotchedwa Minbus Owners Association of Malawi MOM yomwe ife tili nayo yati kukwera mtengo kwa mafuta kwakhuza zedi bizinesi yawo poti pano pali kale lamulo lakuti anthu asamakhale anayi pa mpando umodzi kamba ka muliri wa Covid19 omwe njira imodzi  yofalila ndi kudzera mumpweya omwe anthu amapuma.

Mlembi wa bungweli a Coxley Kamange ati izi ziyambira lero kumapita kutsogoloku, petulo pano akugulitsidwa pa K899 pa lita ndipo Dizilo ali pa K898.

Koma polankhula ndi olemba nkhani, a Bright Msaka omwe amalankhulila chipani cha Democratic Progressive Party DPP pa nkhani zamalamulo ati boma liyenera kupeza njira kuti mafuta akhale ndi mtengo okhadzikika ndipo anapitiliza kunena kuti chiloweleni mu boma a Tonse Alliance, mafuta akungokwera mtengo ndipo boma likupezelapo mwayi pakukwera mtengo kwa mafuta pa dziko lonse kuti aziwabera a Malawi omwe malingana ndi a Msaka ndi osauka ndikale.

Iwo anatinso nthawi ya DPP boma limapeza njira kuti mafuta asakwere mtengo ngakhale kuti mtengo ukwere pa dziko lonse poti iwo amalingalira kaye momwe a Malawi amapezera ndalama.

Advertisement