Mbava zaba ku ofesi ya Chilima

Advertisement

Mbava zathyola ndi kuba katundu wina ku ofesi kwa wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino, komwe ndi amodzi mwa malo omwe kumakhala chitetezo chokhwima kwambiri.

Nkhaniyi watsimikiza ndi Pilirani Phiri yemwe ndi mneneri wa wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino a Saulos Chilima yemwe wati mbava zolimba ntima ngati fiti zazikazizi, Lamulungu lapitali zathyola mbali imodzi ya ofesi ya a Chilima ku Capital Hill.

A Phiri ati anthu amanja ataliataliwa aba kompiyuta ndizipangizo zina za kompiyuta komaso wailesi zomwe zinali mu ofesi yomwe ndimbali imodzi ya ofesi ya wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko ndipo mumakhala yemwe amathandizira a Chilima (director of administration).

Koma funso nkumati ndindani walimba mtima kukaba malo otetezedwa ngati amenewa? Sizikudziwika koma pakadali pano kafukufuku alimkati kufufuza zomwe zachitika kuti mbavazi zikalimbe mtima kuba ku Capital Hill.

Pakadali pano anthu m’masamba amchezo akukamba zosiyanasiyana pamene ena ati mwina umbavawu ukukhudzana ndi komiti yomwe yakhazikitsidwa posachedwapa yomwe wapampando wake ndi Dr Chilima yomwe ikufuna kupanga chipikisheni pankhani ya ma alawasi mmaofesi aboma.

Ena akukamba kuti nkutheka kuti mmodzi mwa anthu ogwira ntchito Ku maofesiwa ndi yemwe wathandizira mbavazi kuti zikwanitse kuba katunduyu.

Advertisement

One Comment

  1. Boma likuziwapo kanthu including mwini wakeyo. Mwacidule nditha kunena kt apanga izi pofuna kusowesa maumboni omwe ali nkatimo. Zitheka bwnj mbava kuthyola/kuba ku Office ya Vice President angankhale President amene,, Kalipo kalipo apa asatinamize ife

Comments are closed.