Aphunzitsi sakayamba ntchito lolemba – TUM

Advertisement

Pomwe boma lalengeza kuti lolemba likubwelari sukulu zonse mdziko muno zitsekulidwe, bungwe la aphunzitsi la Teachers Union of Malawi (TUM) lati aphunzitsi onse apitilirabe kukhala pa tchuthi ngati boma silimva pempho lawo pandalama zaukaziotche.

Malingana ndi mkulu wa bungwe la TUM a Willy Malimba sukulu zonse zisanatsekulidwe lolemba lino, boma likuyenera liwauze kaye tsogolo la nkhani ya ndalama ya ukaziotche yomwe mmbuyomu anapempha kuti azipatsidwa.

A Malimba ati boma likuyenera kumawapatsa aphunzitsi ndalama yaukaziotche kaamba koti miyoyo yawo imakhala pachiopsezo chotenga kachirombo ka corona ati chifukwa choti nthawi ya ntchito yawo amakumana ndi ana osiyanasiyana kotelo kuti mkwapafupi kutenga matendawa.

Iwo ati aphunzitsi ndiodabwa kuti boma likulimbalimba pankhani ya ndalama ya ukazitche yawo chosecho apolisi komaso ogwira ntchito ku ndende akumapatsidwa ndalama zaukadziotchezi.

Aphunzitsiwa atiso akufuna kuti sukulu zisanatsekulidwe, boma likozeletu zinthu zonse zomwe lanena kuti lipanga monga kukumba mijigo mmasukulu onse komaso kupeleka zipangizo zozitetezela zokwanira ku sukulu zonse.

“Ife tikutelo kuti aphunzitsi onse sitipita kukagwira ntchito pamene sukulu zikutsekulidwa lolemba lino chifukwa tikufuna kuti boma litiuze kaye tsogolo la nkhani yokhudza ndalama za ukaziotche,” atelo a Malimba.

A Malimba awonjezeraso kuti aphunzitsi akufunaso apatsidwe ndalama zomwe zinatsala zaukadziotche za mbuyomu ponena kuti m’phunzitsi aliyese ankayenera kulandira K15000 yaukadziotche koma mmalo mwake amalandira K1500 ndipo apempha boma kuti lifufuze nkhaniyi.

Apa Iwo ati akufuna apatsidwe ma K13500 otsalawoo komaso apatsidwe ndalama za miyezi yose yomwe aphunzitsiwa sanalandile ndalama yaukaziotcheyi.

Aphunzitsi ena mumzinda wa Lilongwe, lachisanu mmawa anathamangitsidwa ndi apolisi pomwe amafuna kuchita zionetsero zofuna kukakamiza boma kuti libwere poyera ndikuwauza zomwe zichitike pankhani yokhudza ndalama zaukadziotchezi.

Malingana ndi akuluakulu apolisi, izi zinachitika kaamba koti aphunzitsiwa sanakatenge chilorezo choti apange zionetselozi.

Advertisement