Ndalama za Covid-19: Wachiwiri kwa mkulu wa DODMA wanjatwa

Advertisement

Apolisi mumzinda wa Lilongwe anjata wachiwiri kwa mkulu wanthambi yowona za ngozi zogwa mwadzidzi a Fyawupi Mwafongo kaamba ka ndalama za mlili wa covid-19.

Nkhaniyi ikutsatila kafukufuku yemwe akuchitika zitadziwika kuti ndalama zomwe zimayenera kugwira ntchito pa nkhondo yolimbana and mlili wa Covid-19, zinadyedwa ndi akuluakulu ena aboma makamaka makosana akuti nthambi ya DODMA.

Potsatila kafukufukuyu, Lachiwiri pa 16 February, 2021, apolisi agwira ndikunjata a Mwafongo kaamba kowaganizira kuti akudziwapo kanthu zaku sakazidwa kwa ndalama zankhaninkhani zikunenedwazi.

Watsimikiza zankhaniyi ndi mkulu wofalitsa ku Malawi Police Service a James Kadadzera omwe ati mkuluyu wamangidwa potsatira kafukufuku yemwe apolisi mumzinda wa Lilongwe ayamba kupanga pankhani ya ndalamazi.

A Kadadzera ati a Mwafongo omwe pakadali pano ali mchitokosi cha apolisi, posachedwa akaonekera Ku khothi lomwe akuyembekezeka kukayankha mlandu wakuba pantchito komaso kugwiritsa ntchito ifeso yawo molakwika.

Lamulungu lapitali mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera achotsa paudindo mkulu wanthambi ya DODMA a James Chiusiwa komaso wapampando wa komiti yamtsogoleri wadziko pantchito yothanda ndi mlili wa Covid-19 a John Phuka pankhani yakusakazidwa kwa ndalama zomwezi.

A Chakwera ati a Chiusiwa komaso Dr Phuka, onse alephera pantchito zawo ati kaamba koti kafukufuku wa mkulu omva za madandaulo a anthu pazinthu zosiyanasiyana a Martha Chizuma wasonyeza kuti ndalama zankhaninkhani za Covid-19 zinasakazidwa.

Advertisement